Publicidade

Mateus 26

Yesu mu Getsemani

36 Kenaka Yesu anapita ku malo otchedwa Getsemani, ndipo anawawuza kuti, "Khalani pano pamene Ine ndikukapemphera apo." 37 Anatenga Petro ndi ana awiri a Zebedayo, ndipo anayamba kumva chisoni ndi kuvutika mu mtima. 38 Pamenepo anawawuza kuti, "Moyo wanga uli ndi chisoni chofa nacho. Khalani pano ndipo dikirani pamodzi ndi Ine."

39 Atapita patsogolo pangʼono, anagwa pansi chafufumimba napemphera kuti, "Atate anga, ngati ndikotheka, chikho ichi chichotsedwe kwa Ine. Koma osati monga mmene ndifunira, koma monga mufunira Inu."

40 Kenaka anabwera kwa ophunzira ake nawapeza ali mtulo. Iye anafunsa Petro kuti, "Kodi anthu inu, simukanakhala maso pamodzi ndi Ine kwa ora limodzi lokha? 41 Khalani maso ndi kupemphera kuti musagwe mʼmayesero. Mzimu ukufuna koma thupi ndi lofowoka."

42 Anachokanso nakapemphera kachiwiri kuti, "Atate anga, ngati chikhochi sichingandichoke, mpaka nditamwa, kufuna kwanu kuchitike."

43 Atabweranso anawapeza ali mtulo chifukwa zikope zawo zinalemedwa ndi tulo. 44 Choncho anawasiya napitanso kukapemphera kachitatu nanenanso chimodzimodzi.

45 Kenaka anabwera kwa ophunzira ake nati kwa iwo, "Kodi mukanagonabe ndi kupumula? Taonani, ora layandikira ndipo Mwana wa Munthu akuperekedwa mʼmanja mwa ochimwa. 46 Imirirani, tiyeni tizipita! Wondipereka Ine wafika!"

Veja também

Publicidade
Bíblia Online Bíblia Online

Bíblia Online • Versão: 2026-06-28_14-13-17-