Ascensão
A ascensão de Jesus ao céu é a coroação de sua obra redentora. Ele subiu à destra do Pai, de onde voltará com poder e glória para buscar os seus.
Yapo wadamaliza kukamba chimwecho, Yesu wadanyakulidwa kupita kumwamba uku wonjhe naapenya, ni mtambo udamvinikila kuti saadamuonanjho.
Maso yawo yapo yadali yakali kumpenyechecha kumwamba Yesu yapo wamapita, mwachizulumukila wachimuna awili yawo adavala njhalu zoyela adaima pambhepete pawo, adakamba, "Anyiimwe wandhu a ku Galilaya, ndande yanji muima pamenepo uku nimpenya kumwamba? Yesu uyo watengedwa kupita kumwamba, siwajhenjho ngati mujha mwamuwonela niwapita kumwamba."
Yesu watengedwa kupita kumwamba
Ambuye Yesu yapo adamaliza kukamba ni oyaluzidwa wawo, adatengedwa kupita kumwamba, adakhala kubendeka la kwene la Mnungu.
Yesu watengedwa kupita kumwamba
Ndiipo, Yesu wadaachogoza woyaluzidwa wake kupita mbaka mbhepete mwa mujhi wa Besaniya, pamenepo wadakweza manja yake ni kwapacha mwawi. Yesu yapo wamapacha mwawi, wadatengedwa kumwamba ni kwasiya ni kupita kumwamba.
Munyumba ya Atate wanga muli ni makhalo yambili, ngati siidakali chimwecho, nidakakukambilani. Chipano nipita kukukonjelani malo.
Zene nikukambilani, uyo wanikhulupilila siwachite vindhu ivo nichita ine, ni siwachite vavikulu kupunda, ndande nipita kwa Atate.
Ine nidachoka kwa Atate, nidajha pajhiko, ni chipano nilisiya jhiko nibwela kwa Atate."
Yesu wadamkambila, "Usadanigwila, ndande nikali osapite kumwamba kwa Atate. Nambho mapita kwachabale wanga ukaakambile. Nipita kumwamba kwa Atate wanga ni Atate wanu, Amnungu wanga ni Amnungu wanu."
Chimwecho Yesu wadaakambila, "Nikali namwe kwa ndhawi yo chepa, ndiipo sinipite kwa yujha wanituma.