5Chikhulupiriro ndi chikondi, gwero lake ndi chiyembekezo chomwe muli nacho chodzalandira zimene anakusungirani kumwamba. Munamva kale za zimenezi kudzera mʼmawu a choonadi, Uthenga Wabwino
23ngati mupitirirabe kukhala mʼchikhulupiriro chanu, okhazikika ndi olimba, osasunthidwa kuchoka pa chiyembekezo chimene munachigwira mu Uthenga Wabwino. Uwu ndi Uthenga Wabwino umene munawumva, umene wakhala ukulalikidwa kwa olengedwa onse a pansi pa thambo, ndi umenenso, ine Paulo ndinakhala mtumiki wake.
26chinsinsi chimene chakhala chikubisika kwa nthawi ndi mibado, koma tsopano chawululidwa kwa oyera mtima.