Pular para o conteúdo
Publicidade

HOSEYA 14

Kulapa Kubweretsa Madalitso

1 Iwe Israeli bwerera kwa Yehova Mulungu wako.

Machimo anu ndi amene akugwetsani!

2 Bweretsani zopempha zanu

ndipo bwererani kwa Yehova.

Munene kwa Iye kuti,

"Tikhululukireni machimo athu onse

ndi kutilandira mokoma mtima,

kuti tithe kukuyamikani ndi mawu a pakamwa pathu.

3 Asiriya sangatipulumutse;

ife sitidzakwera pa akavalo ankhondo,

sitidzanenanso kuti, Milungu yathu

kwa zimene manja athu omwe anazipanga,

pakuti ndinu amene mumachitira chifundo ana amasiye."

4 Ine ndidzachiza kusakhulupirika kwawo

ndipo ndidzawakonda mwaufulu

pakuti ndaleka kuwakwiyira.

5 Ndidzakhala ngati mame kwa Israeli

Ndipo iye adzachita maluwa ngati kakombo.

Adzazika mizu yake pansi

ngati mkungudza wa ku Lebanoni;

6 mphukira zake zidzakula.

Kukongola kwake kudzakhala ngati mtengo wa olivi,

kununkhira kwake ngati mkungudza wa ku Lebanoni.

7 Anthu adzakhalanso mu mthunzi wake.

Iye adzakula bwino ngati tirigu.

Adzachita maluwa ngati mphesa

ndipo kutchuka kwake kudzakhala ngati vinyo wochokera ku Lebanoni.

8 Efereimu adzati, "Ndidzachita nawonso chiyani mafano?

Ine ndidzamuyankha ndi kumusamalira.

Ine ndili ngati mtengo wa payini wobiriwira;

zipatso zako zimachokera kwa Ine."

9 Ndani ali ndi nzeru? Adzazindikire zinthu izi.

Ndani amene amamvetsa zinthu? Adzamvetse izi.

Njira za Yehova ndi zolungama;

anthu olungama amayenda mʼmenemo,

koma anthu owukira amapunthwamo.

Estes versículos te tocaram? Ore agora!

+581 estão orando agora.

Junte-se à corrente de oração.

Veja também