Pular para o conteúdo
Publicidade

HOSEYA 3

Hoseya Ayanjana ndi Mkazi Wake

1 Yehova anati kwa ine, "Pita kamukondenso mkazi wako, ngakhale ali pa chibwenzi ndi wina ndi kuti ndi wachigololo. Mukonde iyeyo monga momwe Yehova amakondera Aisraeli, ngakhale iwo amapita kukapembedza milungu ina ndi kukonda nsembe za keke zamphesa zowuma."

2 Motero ndinamukwatira popereka ndalama khumi ndi zisanu zasiliva, ndiponso mitanga isanu ndi iwiri ya barele. 3 Kenaka ndinamuwuza mkaziyo kuti, "Ukhale nane masiku ambiri; usachitenso zachiwerewere kapena chigololo ndi munthu wina, ndipo ine ndidzakhala nawe."

Veja também