12 Ndinawawuza kuti, "Ngati mukuganiza kuti zili bwino, patseni malipiro anga; koma ngati si choncho, sungani malipirowo." Kotero anandipatsa ndalama zasiliva makumi atatu.
13 Ndipo Yehova anandiwuza kuti, "Ziponye kwa wowumba mbiya," mtengo woyenera umene anapereka pondigula Ine! Choncho ndinatenga ndalama zasiliva makumi atatu ndi kuziponya mʼnyumba ya Yehova kwa wowumba mbiya.