Amor verdadeiro
O amor verdadeiro vem de Deus. Não é emoção passageira — é decisão, sacrifício e compromisso eterno. O perfeito amor lança fora o medo e nunca deixará de existir.
Mateyake Amnungu adaakonda wandhu a jhiko la panjhi ni kumchocha Mwana wao wa yokha, kuti kila uyo wamkhulupilila siwadatayika, nambho wakhale ni umoyo muyaya.
Nikupachani lamulo la chipano, ngati umo nakukondelani anyiimwe, namwenjho mkondane mwachinawene kwa mwachinawene. Mkakondana, wandhu onjhe sajhiwe kuti anyiimwe nde oyaluzidwa wanga."
Nambho Mnungu wachimikiza kuti watikonda, pakuti yapo tidali tikali amachimo, kilisito wadafa ndande yathu.
Pakuti nijhiwa uzene kuti palibe chindhu chikhoza kutipatula ni chikondi cha Mnungu ikhakhala nyifa kapina umoyo, kapina atumiki a akumwamba kapina mbhavu zina za kumwamba, kapina yayo yachokela saino, kapina yayo siyachokele pambuyo, kapina ulamulilo, kapina jhiko la kumwamba kapina jhiko la panjhi kupunda. Palibe choumbidwa chalichonjhe chikhoza kutiika patali ni chikondi cha Mnungu mkati mwa Kilisito Yesu mbuye wathu.
Uyo wamkonda mnjake siwakhoza kumchitila chindhu choipa. Chimwecho chikondi nde kuvela thauko lonjhe.
Uyo wali ni chikondi waembekeza, wathangatila, uyo wali nichikondi walibe njhanje, walibe dama, kapina kujhiona, uyo wali ni chikondi siwachepa ulemu, uyo wali ni chikondi siwafuna vindhu va kumthangatila mwene, kapina mbhwai za msanga, siwasunga chikumbukilo cha voipa, mundhu wa chikondi siwakondwela voipa, nambho chikondwela uzene. Mundhu wachikondi wapilila yonjhe, mundhu wa chikondi wakhulupila wina, mundhu wa chikondi waembekeza, ni siwalepela.
Chikondi chiendekela sikuzonjhe, nambho ukakhalapo ulosi siuthele, ikakhalapo mikambo siithela kukakhalapo kujhiwa nako sikuthele.
Nambho ivo vichokela ukachogozedwa ni Mzimu wa Mnungu ni chikondi, kukondwela, mtendele, kulimba mtima, ubwino, kutangatila wina ni kukhulupilika,