Milagres de Jesus
Os Evangelhos registram dezenas de milagres realizados por Jesus — curas, ressurreições, domínio sobre a natureza e libertações. Cada milagre revelava sua divindade e compaixão.
Curas de cegos e surdos
Jesus devolveu a visão aos cegos e a audição aos surdos, manifestando seu poder sobre toda enfermidade e deficiência.
Yesu waalamicha osapenya awili
Yesu yapo wamachoka pamalo pamenepo, yapo wadali mnjila, osapenya awili adamchata, adakamba, "Mwana wa Daudi, utilengele lisungu!"
Yesu yapo wadalowa mnyumba, wajha osapenya awili adamchata, wadaafunjha, "Bwanji, mkhulupilila kuti nikhoza kukulamichani?"
Anyiiwo adamuyangha, "Yetu, Ambuye."
Yesu wadaagafya maso yao, wadakamba, "Ikhale chimwecho ngati umo mukhulupilila." Maso yao yadakhoza kupenya. Yesu wadakaniza kupunda, "Msadamkambila mundhu waliyonjhe vindhu ivi!"
Nambho anyiiwo adachoka, adaeneza nghani za Yesu mujhiko lonjhe lijha.
Yesu waalamicha osapenya awili
Yesu ni oyaluzidwa wake yapo amachoka kumujhi wa Yeliko, gulu lalikulu la wandhu lidamchata. Osapenya awili adakhala mmbhepete mwa njila. Yapo adavela kuti Yesu wapita pamenepo, adabula phokoso niakamba, "Ambuye, Mwana wa Daudi, tilengele lisungu!"
Gulu lijha lidaanyindila ni kwaakambila akhale chete. Nambho anyiiwo adayendekela kutanilila niakamba, "Ambuye, Mwana wa Daudi, tilengele lisungu!"
Yesu wadaima ni kwaatana, wadaafunjha, "Mfuna nikuchitileni chiyani?"
Adamuyangha, "Ambuye, tifuna kupenya!"
Yesu wadaalengela lisungu ni wadaagafya maso yao. Pampajha adakhoza kupenya, nawo adamchata.
Yesu wamlamicha mundhu wosapenya ku Betisaida
Yesu ni oyaluzidwa wake adafika kumujhi wa Betisaida, wandhu adampelekela mundhu uyo siwamapenye, adampembha kupunda wamgafye kuti wamlamiche. Yesu wadamgwila yujha mundhu jhanja, ni kumtulucha kubwalo kwa mujhi. Ndiipo wadamlavulila malovu mmaso, wadamuikila manja ni kumfunjha "Bwanji, uona chiyani?" Yujha mundhu wadapenya ni kukamba, "Niona wandhu ali ngati mitengo niayenda." Ndiipo, Yesu wadamuikilanjho manja mmaso, ni maso yake yadamasuka, wadaona bwino kilakandhu. Yesu wadamkambila wabwele kukhomo lake ni kumlamula, "Siudalowa mkati mmujhi!"
Yesu wamlamicha bubu gondhi
Wadachoka mmujhi wa Tilo ni kupita ku Sidoni mbaka ku nyanja ya Galilaya ni kufika pamalo pa Dekapoli, mate yake mijhi khumi. Kumeneko, wandhu adampelekela bubu gondhi kwa Yesu, ni adampembha kupunda wamuikile manja kuti wamlamiche. Yesu wadamchocha yujha bubu gondhi kumbhepete kwa wandhu ni wadamuikila vyala mmakutu, wadalavula malovu ni kuligafya lilime la yujha mundhu. Wadapenya kumwamba, wadapuma kwa mbhavu ni kumkambila, "Efata" mate yake, "Masuka." Pampajha, makutu yake yadamasuka, ni lilime lake nalo lidalenda, wadayamba kukamba bwino. Ndiipo Yesu wadaalamula asadamkambila mundhu waliyonjhe nghani zijha. Nambho umo wadapunda kwaakanizila, nde umo adayendekela kuziyeneza zijha nghani. Wandhu adazizwa kupunda nikukamba, "Wavichita ivi vonjhe bwino, wamkhozecha agondhi kuvela, ni mabubu akambe!"
Yesu wamlamicha mudhu wosapenye Batimayo
Ndiipo, adafika ku Yeliko. Yesu ni oyaluzidwa wake pamojhi ni gulu lalikulu la wandhu, adampheza mundhu mmojhi wosapenya, uyo wamatanidwa Batimayo, mwana wa Timayo, wakhala pambhepete pa njila niwapembha pembha vindhu. Batimayo yapo wadavela kuti Yesu wa ku Nazaleti wamapita pamalo yameneyo, wadakweza mvekelo wake, niwakamba, "Imwe a Yesu, Mwana wa Daudi nilengeleni lisungu!" Wandhu ambili adamnyindila, adamkambila wakhale chete, nambho iye wadapunda kukweza mvekelo, "Imwe Mwana wa Daudi, nilengeleni lisungu"
Yesu wadaima, ni kukamba "Mkambileni wajhe." Ndiipo adamtana, adamkambila, "Jhipache mtima, ima watokutana." Niiye wadataya kutali njhalu yake, wadalumbha ni kumpitila Yesu.
Yesu wadamfunjha, "Ufuna nikuchitile chiyani?" Sapenya yujha wadamuyangha, "Oyaluza, nipemhba nipenye."
Yesu wadamkambila, "Pita, kukhulupilila kwako kwakulamicha." Pampajha, yujha sapenya wadakhoza kupenya, ndiipo wadamchata Yesu mnjila.
Yesu wamulamicha mundhu wosapenya
Yapo Yesu wadali pafupi kufika ku Yeliko, wadakomana ni mundhu mmojhi wosapenya, uyo wadakhala mbhepete mwanjila kupembhapembha. Yapo wadavela wandhu ambili niapita, wadafunjha, "Kuli chiyani?" Adamuyangha, "Yesu wa ku Nazaleti watopita." Ndiipo wosapenya mmeneyo wadakweza mvekelo, wadakamba, "Yesu Mwana wa Daudi, unilengele lisungu!" Anyiwajha adali mchogolo adamnyindila kuti wakhale chete. Nambho iye wadaendekela kukweza mvekelo waukulu, "Mwana wa Daudi chonde, unilengele lisungu!" Yesu wadaima ni kwalamula kuti ajhenayo kwaiye. Wosapenya yujha yapo wadafika pafupi, Yesu wadafumnjha, "Ufuna nikuchitile chiyani?" Iye wadayangha, "Ambuye nifuna nikhoze kupenya." Yesu wadamuyangha, "Penya, chikhulupililo chako chakulamicha." Pampajha mundhu yujha wadakhoza kupenya, wadamchata Yesu uku niwamkweza Mnungu. Yapo adaona chimwecho, wandhu wonjhe adamtamanda Mnungu.
Yesu wamlamicha mundhu uyo wabadwa osapenya
Siku limojhi Yesu yapo wamapita wadamuona mundhu mmojhi, uyo siwapenya kuyambila kubadwa kwake. Basi oyaluzidwa wake adamfunjha, "Oyaluza! Yani wachita machimo, mundhu uyu kapina obala wake, mbaka wabadwe osapenye?"
Yesu wadaayangha, "Wabadwa osapenye osati ndande ya machimo yake, kapina ya obala wake, wadabadwa chimwecho kuti mbhavu ya Amnungu iwoneke muumoyo wake. Ifunika tiendekele kuzichita njhito za yawo atituma kukali usana, ndande usiku ukujha uwo mundhu waliyonjhe siwakhoza kuchita njhito. Ndhawi nili pano pajhiko, ine nde dangalila la wandhu a pajhiko."
Yapo wadakamba chimwecho, wadalavula malovu panjhi, wadakonja thokope, wadamnyeka yujha osapenyeyo mmaso, wadamkambila, "Pita ukasambe kuthiwi la Siloamu." Mawu Siloamu mate yake Uyo watumidwa. Chimwecho wadapita kusamba, wadabwela uku ni wapenya.
Curas de paralíticos e enfermos
Paralíticos caminharam, leprosos ficaram limpos e todo tipo de doença foi curada pelo toque e pela palavra de Jesus.
Mundhu mmojhi uyo wadali ni makate wadamchata Yesu, wadamgwadila ni kukamba, "Ambuye, mkafuna, mkoza kunilamicha kuti nikhoze kumlambila Mnungu!"
Yesu wadatambasula jhanja lake, nikumgafya wodwalayo ni kumkambila, "Nifuna! Ulame." Pampajha mundhuyo wadalama makate yake. Ndiipo Yesu wadamkambila, "Vechela, usadamkambila mundhu waliyonjhe, nambho pita ukajhilangize kwa ajhukulu, ni kuchocha njhembe iyo yalamulidwa ni Musa kuwachimikhizila wandhu wonjhe kuti walama."
Kumeneko adampelekela mundhu ovuwala uyo wadagona pachitala. Yesu yapo wadaona chikulupi chao, wadamkambila mundhu yujha ovulala, "Limba mtima mwana wanga! Walekeledwa machimo yako!"
Akumojhi awoyaluza mathauko amakambilana achinawene, "Mundhu uyu wamchita chipongwe Mnungu!"
Yesu wadajhiwa ivo amakambilana, wadafunjha, "Bwanji, ndande yanji mkambilana voipa? Liti lili lopepuka, kukamba, ‘Walekeleledwa machimo yako,’ kapina kukamba, ‘Ima uyende?’ Chipano nifuna mjhiwe kuti Mwana wa Mundhu wali nilamulo mujhiko lakulekelela machimo ya wandhu." Pamwepo wadamkambila yujha mundhu ovulala, "Ima, tenga chitala chako, ujhipita kukhomo kwako!"
Pampajha Yujha mundhu wadavula wadaima ni kupita kukhomo lake.
Mmenemo mdali ni mundhu mmojhi wavulala jhanja. Ndiipo Afalisayo wina adamfunjha Yesu, "Bwanji, ni bwino kumlamicha mundhu Siku Lopumulila?" Adamfunjha chimwecho kuti apate ndande yakumgwilila.
Yesu wadaakambila, "Tikambe mmojhi wanu wali ni mbelele iyo yabila mjhenje lonyowa, bwanji siwaichuula mujha mjhenje Siku Lopumulila? Mundhu wali mbasa kupitilila mbelele! Chimwecho tifunika kuchita vindhu vabwino pa Siku Lopumulila." Ndiipo Yesu wadamkambila yujha mundhu, "Tambasula jhanja lako."
Wadatambasula, nalo lidalama ni kukhala ngati jhanja lina lijha.
Apongozi wake waakazi a Simoni, adali agona pachika niadwala homa. Yesu yapo wadafika, adamkambila nghani za wodwala mmeneyo. Yesu wadaasendelela wajhja maye, nikwaagwila jhanja, wadaanyakula. Ni homa idamchoka, wadayamba kwatumikila.
Yesu wamulamicha mundhu makate
Mundhu mmojhi uyo wadali ni makate wadampitila Yesu, wadamgwadila wadampembha, wadakamba, "Ukafuna ukhoza kuniyelecha, kuti nikhoze kumlambila Mnungu!" Yesu wadamlengela lisungu mundhu mmeneyo, wadatambasula jhanja lake ni wadamgafya, kumkambila, "Nifuna, uyelechedwe!" Pampajha makate yadamchoka mundhu mmeneyo, nayo wadalama.
Pamenepo, adafika wandhu anayi, adamtenga mundhu wovuwala, adampeleka kwa Yesu. Saadakhoze kumpeleka pafupi ni Yesu ndande ya lijha gulu la wandhu. Chimwecho adakwela pamwamba, adafulumula chindu, pajha wadali Yesu. Yapo adafulumula, adamchicha mundhu yujha uku amgoneka pa chitala. Yesu yapo wadaona chikhulupililo chao, wadamkambila yujha mundhu wovuwala, "Bwenji langa, nakulekelela machimo yako." Woyaluza akumojhi athauko la Musa, yawo adali pamenepo adaganizila mmitima yao, "Chindhu chanji icho chimkhozecha kukamba chimwechi? Wamkafula Mnungu! Ni Mnungu yokha uyo wakhoza kulekelela machimo." Pampajha, Yesu wadayajhiwa yayo amaganizila mmitima yao, wadaakambila, "Bwanji mganiza chimwecho? Nichiti chili chopepuka kupunda, kumkambila mundhu uyu wavuwala, ‘Walekeledwa machimo yako,’ kapina kumkambila, ‘Uka, utenge chitala chako upite?’ Chipano, nifuna mjhiwe kuti ine Mwana wa Mundhu nali ni ulamulilo wolekelela machimo ya wandhu pajhiko." Pamenepo, wadamkambila yujha mundhu wadavuwala, "Nikukambila, uka utenge chitala chako, upite kukhomo!"
Pampajha yujha wodwala wadauka, wadatenga chitala chake ni kuchoka, uku wandhu wonjhe niampenya. Wandhu wonjhe adazizwa ni kumtamanda Mnungu, niakamba, "Sitidaonepo chindhu ngati ichi."
Yesu wamlamicha mundhu pa Siku lo Pumulila
Ndiipo Siku lina lo Pumulila, Yesu wadalowanjho mnyumba yokomanilana Ayahudi, ni mujha mkati kudali ni mundhu uyo wali ni jhanja lovuwala. Mmenemo, kudali Afalisayo akumojhi yawo amampenya amuone ngati samlamiche mundhu Siku lo Pumulila apate ndande ya kumgwila. Yesu wadamkambila yujha mundhu wadali ni jhanja lovuwala, "Majha pano pakatikati." Ndiipo wadaafunjha wandhu, "Bwanji, mathauko ya Musa yatifuna tichite chiyani pa Siku lo Pumulila? Bwanji, kuchita vabwino kapina kuchita voipa? Kuuwombola umoyo wa mundhu kapina kuupha?" Nambho anyiiwo adakhala chete. Yesu wadaapenya wonjhe kwa mbhwayi, pamenepo wadaona chisoni mumtima mwake ndande ya kosakhulupilila kwawo. Ndiipo wadamkambila yujha mundhu, "Tambasula jhanja lako." Ni yujha wovuwala wadatambasula jhanja lake, ni kulama.
Yesu wamulamicha mundhu wa vizunguluta
Ndhawi iyo Yesu wadali mu mujhi umojhi pakati pa mijhi yakumeneko, ni kumeneko kudali ni mundhu mmojhi uyo wadali vizunguluta thupi lambhumbhu. Yapo wadamuona Yesu wadagwada ni kumkwatamila, niwakamba, "Ambuye, mukafuna mkhoza kunilamicha kuti nikhoze kumlambila Mnungu." Yesu wadatambasula jhanja lake ni kumgafya wodwalayo, nikumkambila, "Nifuna, ulame kuti ukhoze kumlambila Mnungu!" Ndhawi imweyo utenda udamchoka mundhu yujha.
Wandhu wina adajhanayo mundhu wopuwala uyo adamgoneka pachitala. Adayesa kumlovya mkati mwa nyumba ni kumgoneka pamaso pa Yesu. Yapo adalepela kumlovya mkati ndande ya kuchuluka kwa wandhu, adakwela pachindu ni kufulumula chindhu apate malo ya kumchichila pamojhi ni chitala pakati pa wandhu pamaso pa Yesu. Yapo Yesu wadaona chikhupililo chao, wadamkambila wodwala yujha, "Bwenji, walekeleledwa machimo yako."
Oyaluza a thauko ni Afalisayo adayamba kujhifunjha achinawene wake, "Mundhu uyu ni yani mbaka wamkhafule Mnungu? Palibe mundhu uyo wakhoza kwaalekelela wandhu machimo yao nambho Mnungu yokha!" Nambho Yesu wadajhiwa maganizo yawo ni wadaafunjha, "Ndande yanji mujhifujha chimwecho mmitima yanu? Chiti icho chili lahisi kupunda, kukamba, ‘Walekeleledwa machimo yako.’ Kapina kukamba, ‘Ima ujhiyenda?’ Chipano nifuna mjhiwe kuti Mwana wa Mundhu wali ni ulamulilo wa kwalekelela wandhu machimo yao pano pajhiko." Pamwepo wadamkambila mudhu yujha wopuwala, "Ima, ni utenge chitala chako, upite kukhomo lako."
Ndhawi imweyo mudhu wopuwala yujha wadaima pamaso ya wandhu wonjhe, wadatenga chitala chake icho wamagonela nikupita kukhomo lake, uku niwamtamanda Mnungu.
Yesu wamlamicha Mundhu wa jhanja lopuwala
Siku lina lopumulila, Yesu wadalowa mu nyumba yokomanilana Ayahudi, kuyaluza. Mkati mujha mudali mundhu mmojhi wopuwala jhanja la kwene. Oyaluza thauko ni Afalisayo amatokumpenyechecha yesu kuti aone ngati siwamlamiche mundhu siku lo pumulila, kuti nianyiiwo akhoze kumpacha mlandu. Nambho Yesu wadajhiwa maganizo yao. Chimwecho wadamkambila mundhu yujha wa jhanja lopuwala, "Nyakuka, ima pachogolo pa wandhu." Ni yujha mundhu wadapita kuima pachogolo pajha. Ndiipo Yesu wadaakambila oyaluza thauko ni Afalisayo, "Nikufunjhani anyiimwe, bwanji, ni bwino siku lopumulila kuchita vindhu vabwino kapina kuchita vindhu voipa? Bwanji tikhoza kulamicha umoyo wa wandhu kapina kuyapha?" Wadaapenyechecha konjhekhonje, ndipo wadamkambila mundhu yujha wopuwala jhanja, "Tambasula jhanja lako!" Niiye wadatambasula jhanja lake, nalo lidapata mbhavu.
Chikhulupililo cha wamkulu wa asilikali wa Loma.
Yesu yapo wadamaliza kwakambila wandhu mawu yameneyo, wadachoka kupita ku Kapenaumu. Kumeneko kudali wamkulu wa gulu la asilikali mwina uyo wadali ni mbowa wake uyo wamamkonda kupunda. Mbowa mmeneyu wadali wodwala pafupi kumwalila. Wamkulu wa asilikali yujha yapo wadavela nghani za Yesu, wadaatuma azee wina wa Ayahudi, apite akampemphe kuti wamlamiche mbowa wake. Yapo adafika kwa Yesu, adampempha kupunda, pokamba, "Mundhu uyu wafunikadi wathangatilidwe, pakuti walikonda jhiko latu, ni iye watimangila, nyumba yopezanilana." Ndiipo, Yesu wadapita pamojhi naanyaiwo. Yapo adawandikila kufika pakhomo pa yujha wamkulu wa asilikali, wamkulu wa gulu la asilikali wadaatuma achabwenji wake kwaiye amkambile, "Ambuye, msadajhichaucha kupunda, ndande ine siniloledwa kukulovyani imwe mnyumba mwanga. Ndendande sinidajhione kuti ine nikhoza kujha kwanu imwe. Nambho kambani mawupe, ni mbowa wanga siwalame. Pakuti inenjho ni mundhu uyo nili panjhi pa lamulo, ni nili ni asilikali panjhi panga, yao avela icho naakambila. Nikamkambila mmojhi, ‘Pita,’ iye wapita. Ni wina nimutana, ‘Majha,’ Nayonjho wakujha. Ni mbowa wanga nikamkambila, ‘Chita chimwechi,’ nayonjho wachita."
Yesu yapo wadavela chimwechi wadazizwa, naye wadang’anamukila wandhu ambili yawo amamchata ni kwakambila, "Sinidaonepo chikhulupililo chachikulu ngati ichi ata pakati pa wandhu a Yelusalemu."
Wandhu wajha adatumidwa kwa Yesu, yapo adafika kukhomo kwa wamkulu wa asilikali adampheza mbowa wake watholama.
Mnyumba mmenemo mudali wamkazi mmojhi uyo wamalamulidwa nichiwanda pavyaka khumi ni nane. Nayo wadali nichipindi, nisiwamakhoze kuima. Yesu yapowadamwona wamakazi mmeneyo, wadamtana, ni wadamkambila, "Wamkazi, wamasulidwa chipindi chako." Yesu yapo wadamwikila manja pamwamba pa mutu wake kwa kughafya, ghafula thupi lake lidakhululukanjho, wadayamba kumtamanda Mnungu.
Yesu wamlamicha mundhu wadatupa thupi lonjhe
Siku limojhi Lopumula, Yesu yapo wadalalikidwa kupita kudya chakudya kunyumba ya achogoleli mmojhi wa Afalisayo, uku wandhu na amatomnyemelela. Pachogolo pa Yesu padali mundhu mmojhi uyo wadali ni utenda wothupa thupi. Yesu wadafunjha woyaluza thauko ni Afalisayo, "Bwanji, ni bwino kulamicha wandhu siku Lopumula kapina notho?" Nambho anyiiwo adakhala chete. Chimwecho, Yesu wadamgwila janja ni kumlamicha, ni kumkambila wapite kukhomo lake.
Yesu walamicha amakate khumi
Yesu ni oyaluzidwa wake yapo wadali paulendo wopita ku Yelusalemu, wapitila malile ya Samaliya ni Galilaya. Yapo wamapita mu chijhijhi chimojhi, wadakomana ni wandhu khumi adamjhela Yesu ni adaima patali. Adakweza mvekelo, "Ambuye Yesu, tilengeleni lisungu!" Yesu yapo wadaaona amakate wajha, wadaakambila, "Pitani mkajhilangize kwa ajhukulu." Yapo adali akali mnjila, adalama utenda ni kuvomelezeka kwa chikhalidwe cha kumlambila Mnungu. Mmojhi wao yapo wadaona kuti walama, wadabwelela kwa Yesu uku niwamtamanda Mnungu kwa mvekelo waukulu. Wadagwa chifufumimba mmiyendo ya Yesu ni kumuyamika. Mundhu mmeneyo wadali Msamaliya. Yesu wadamfunjha, "Bwanji, osati wandhu khumi yao adalamichidwa ni kuvomelezeka kwa chikhalidwe cha kumlimbila Mnungu? Bwanji, anyiwajha tisa alikuti? Bwanji, padalibe ata mmojhi uyo wadabwela kumpacha ulemu Mnungu, nambho uyu mlendope?" Ndiipo Yesu wadamkambila mundhu yujha, "Ima ujhipita, chikhulupililo chako chakulamicha."
Yesu wamlamicha mundhu wovuwala Siku lo Pumulila
Pambuyo pa yameneyo kudalipo ni phwando la Ayahudi, nayo Yesu wadapita Ku Yelusalemu. Kumeneko ku Yelusalemu, pafupi ni chicheko icho chitanidwa chicheko cha mbelele, kudaliko ni thiwi ilo kwa mkambo wa Chihebulaniya, Betizata, ilo lidazungulilidwa ni khumbi zisano. Mkati mwake mudali odwala ambili, osapenya, andendele, ni ovuwala. Amalindilila majhi yavundulidwe, pakuti ndhawi za mbili mtumiki wa kumwamba wa Amnungu wamachika ndhawi zina ni kuyavundula majhi. Mundhu waliyonjhe uyo wachogolela kubila mmajhi yayo yamavundulidwa, wamalama ndhenda yaliyonjhe iyo wamadwala. Ndiipo, pamwepo wadalipo mundhu mmojhi uyo wadali odwala kwa ndhawi ya vyaka selasini ni nane. Yesu yapo wadamuona mundhu mmeneyo wagona pamenepo ni kujhiwa kuti wadakhala kwa ndhawi ya itali, wadamfunjha, "Bwanji, ufuna kulama?"
Nayo wadayangha, "Wakulu, ine nilibe mundhu onibiza mthiwi majhi yapo yavundulidwa. Yapo niyesa kulowa, mundhu mwina wanichogolela."
Yesu wadamkambila, "Ima tenga chika lako ujhiyenda." Pampajha mundhu mmeneyo wadalama, wadatenga chika lake ni kuyamba kuyenda.
Chindhu ichi chidachitika Siku lo Pumulila.
Chimwecho Yesu wadafikanjho mbaka Kukana ya ku Galilaya, kujha wadang’anamula majhi kukhala divai. Kudalipo mchogoleli mmojhi uyo wadali ni mnyamata wake uyo wamadwala kujha ku Kapelinaumu. Chimwecho mchogoleli yujha yapo wadavela kuti Yesu wafika ku Galilaya kuchokela ku Yudea, wadamchota ni kumpembha wakamlamiche mwana wake uyo wamadwala pafupi kumwalila. Yesu wadamkambila, "Ukalepela kuona vizindikilo ni vodabwicha siukhulupilila."
Mchogoleli mmeneyo wadamkambila, "Waakulu, pepani tiyeni mwana wanga wakali osafe."
Ndiipo Yesu wadamkambila, "Mapita pe, mwana wako walama."
Yujha mundhu wadakhulupilila mawu ya Yesu ni kupita. Yapo wadali mnjila wadapezana ni mbowa zake, zidamkambila, "Mwanawako walama!"
Chimwecho wadafunjha ndhawi iyo mwana wadalama, adamkambila kuti, "Jhulo ndhawi ya saa saba za usana, nde yapo wadalama." Ndiipo atate wake mwanayo adakumbukila kuti, ndhawi idali ijha Yesu wadamkambila, "Mwana wako walama." Ndiipo iye ni achabale wake onjhe apakhomo lake adakhulupilila.
Ichi chidali chizindikilo chakawili icho wadachichita Yesu, yapo wamachoka ku Yudea kupita ku Galilaya.
A mulher com fluxo de sangue
Uma mulher que sofria há doze anos tocou a orla do manto de Jesus e foi curada instantaneamente pela sua fé.
Yapo amapita maye mmojhi uyo wamasusa nghole kwa vyaka khumi ni viwili, wadamchata Yesu mmbuyo, wadagafya njhonga ya njhalu ya Yesu. Wadaganizila mumtima mwake, "Nikagafyape njhalu yake, sinilame."
Yesu wadapenya mmbuyo wadamwona wamkazi yujha, wadamkambila, "Mwali, limba mtima! Chikulupi chako chakulamicha." Pampajha wamkazi yujha wadalama.
Pajha pagulu wadalipo ni wamkazi uyo wamadwala utenda wosusa nghole kwa vyaka khumi ni viwili. Wamkazi mmeneyo wadavutika kupunda kwakupita kwa asing’anga ambili ni wadatumia chuma chake chonjhe, nambho siwadalame, ni wadaendendekela kudwala kupunda. Wamkazi yujha yapo wadavela nghani za Yesu, wadapekenyela paghulu la wandhu, wadampitila Yesu kwa kumbuyo ni kugafya njhalu yake. Wadajhikambila mumtima mwake, "Nikagafyape njhalu yake, sinilame." Yapo wadagafyape njhalu ya Yesu, pampajha nghole idasiya kususa, nayo wadajhivela thupi lake lalamilatu.
Basi pakati pa gulu la wandhu wajha, padali wamkazi mmojhi uyo wamasusa nghole kwa ndhawi ya vyaka khumi ni viwili, ingakhale wadathowananga chuma chake chonjhe icho wadalinacho kwa masing’anga, nambho palibe uyo wadakhoza kumlamicha. Wamkazi yujha wadajha kumbuyo kwa Yesu ni kugafya njhonga ya chivalo chake, ndhawi imweyo nghole yake idasiya. Yesu wadafunjha, "Yani uyo wanigafya ine?" Wandhu wonjhe adakana. Ni Petulo wadakamba, "Ambuye, ambili akuzungulilani ni kukuzengani!" Nambho Yesu wadakamba, "Pali mundhu wanigafya, najhiwa ndande naona mbhavu zanga zanichoka." Wamkazi yujha yapo wadaona kuti siwakoza kujibisanjho, wadatulukila uku niwatendhemela kwa mandha, wadagwa chifufumimba pamaso pa Yesu. Pamenepo wadafotokoza kwa wandhu wonjhe chifuko cha kumgafyila Yesu ni umo walamichidwila kwankamojhi. Yesu wadamkambila, "Mwali, chikuluphililo chako chakulamicha. Pita kwa mtendele."
Ressurreições
Jesus ressuscitou mortos — a filha de Jairo, o filho da viúva de Naim e Lázaro. Ele é Senhor sobre a morte.
Mwali wa wamkulu ni wamkazi mmojhi alamichidwa
Yesu yapo wamakamba yameneyo, wamkulu mmojhi wa Ayahudi wadamgwadila, ni kukamba, "Mwana wanga wa mwalilila chipano yapa. Nambho, nikupembha ujhe ni umsanjike manja, nayo siwakhale wamoyo."
Yesu wadachoka pamojhi ni oyaluzidwa wake, adachatana ni yujha wamkulu.
Ndiipo Yesu wadalowa uti mnyumba ya wamkulu yujha. Yapo wadaona wandhu yawo amaliza vitolilo va nyimbo za zaya, wadaakambila, "Chokani kubwalo! Mwaliyu siwadamwalile, nambho wangogonape." Anyiiwo adamseka. Yapo adatuluchidwa kubwalo, Yesu wadalowa mnyumba, wadamgwila jhanja mwali yujha, nayo wadaima.
Mmojhi wa achogoleli anyumba yokomanilana Ayahudi uyo wamatanidwa Yailo wadajha pamenepo, niiye yapo wadamwona Yesu wadamgwadila, wadampemba niwakamba, "Mwali wanga wadwala pafupi kumwalila. Chonde nikupembha majha umuikile manja nawo wakhoze kulama ni kukhala wamoyo." Chimwecho Yesu wadapita pamojhi niiye. Ni gulu lalukulu la wandhu limamchata, uku ni niabwanyizabwanyiza.
Yapo adafika kukhomo kwa Yailo, Yesu wamavela mapokoso ni vililo. Yesu wadalowa mkati, wadaafunjha "Bwanji mbula pokoso ni kulila? Mwana siwadamwalile, nambho wagonape." Nambho wandhu wajha adamseka. Chimwecho wadaachocha kubwalo, wadaatenga atate ni amake wa yujha mwali, ni wajha oyaluzidwa wake yawo wadali nawo, adalowa kuchumba chijha adagoneka chitanda chayujha mwali. Yesu wadamgwila jhanja, wadamkambila, "Talisa khumi!" Mate yake, "Mwali, nikukambila uka!" Pampajha yujha mwali wadaima, ni kuyamba kuyenda, mwali yujha wadali ni vyaka khumi ni viwili. Chindhu chimenecho yapo chidachokela, obala ni wajha oyaluzidwa adalowa mujha adazizwa kupunda.
Yesu wadayendekela kukamba, "Bwanji, sinalinganiche ni chiani, wandhu a mbadwa uno? Bwanji, wandhu anyiyawa ni amtundu wanji? Ali ngati wana wokhala pamalo yayo amakomanilana wandhu, naatanana achinawene kwa achinawene wake,
‘Takutimbilani vitolilo, nambho simudavine!
Takuyimbilani nyimbo za zaya nambho simudalile!’
Pakuti Yohana mbatizi yapo wadafika, niwamanga kudya ni wosamwe divayi kila ndhawi, ni anyiimwe mudamnena kuti, ‘Wali ni viwanda!’ Nayenjho mwana wa Mundhu wafika, wakudya ni wakumwa, namwe mkambanjho, ‘Muoneni uyu! Waludyo ni wolojhela, bwenji wa wolandila malipilo ni wochimwa!’ Nambho, ekima ya Mnungu yavomelezewa kuti ni yabwino kwa wonjhe yawo ayivomela."
Yesu wanyekedwa mafuta ni wamkazi wochimwa
Siku limojhi, mfalisayo mmojhi wadamlalika Yesu kujha kudya chakudya cha ujhulo cha mnyumba mwake. Yesu nayonjho wadalowa mnyumba mwa mfalisayo yujha, wadakhala pa chitembwe ni kudya chakudya. Ndiipo, mmujhi ujha mudali wamkazi mmojhi uyo wadali wochimwa. Yapo wadavela kuti Yesu watokudya mnyumba ya mfalisayo, wadatenga njhupa iyo lidajhala mafuta yonunghila.
Pamenepo wadafika mundhu mmojhi uyo wamatanidwa Yailo, uyo wadali mchogoleli wa nyumba yophezelana Ayahudi. Wadafika ni kugwada pa miyendo ya Yesu ni kumpembha wapite kukhomo kwake, pakuti mwali wake wayokha wa vyaka ngati khumi ni viwili wadali kudwala pafupi kumwalila.
Yesu yapo wamapita gulu la wandhu amamzenga kupunda.
Yapo Yesu wadali wakali kukamba, wadafika mundhu mmojhi kuchokela kukhomo kwa mchogoleli yujha ni kumkambila Yailo, mchogoleli wa nyumba ya yokomanilana ayahudi, "Mwana wako wamkazi wamwalila, usadayendekela kumsaucha woyaluza." Nambho Yesu yapo wadavela chimwecho wadamkambila Yailo, "Usadaopa, ungokhulupilila, mwali wako siwalame."
Yesu yapo wadafika kukhomo kwa Yailo, siwadamulole mundhu ata mmojhi kulowa nawo mnyumba mmenemo ingakale Petulo ni Yohana ni Yakobo ni obala amwali yujha. Ndhawi imeneyo wandhu wonjhe amatolila ni kuimba zaya. Nambho Yesu wadakambila, "Msadalila, pakuti mwali uyu siwadafe, nambho wangogonape!" Anyiiwo adamseka kwa kumdelela, pakuti adajhiwa kuti mwali yujha wamwalila. Nambho Yesu wadamgwila janja mwali yujha ni kukamba, "Mwali, nyakuka!" Umoyo wake udambwelela ni wadanyakuka ndhawi imweyo nikukalanjho wamoyo. Ni Yesu wadakambila obala wake kuti ampache chakudya. Obala wake adazizwa kupunda, nambho Yesu wadalamula kuti asadamkambila mudhu waliyonjhe pa ivo vachokela.
Kumwalila kwa Lazalo
Padali ni mundhu mmojhi wa ku Besania, wamatanidwa Lazalo, wamadwala. Wamakhala kuchijhijhi cha Besania kumeneko amakhala ni achalongo wake Malia ni Masa. Malia uyu nde yujha wadaanyeka Ambuye mafuta ya mtengo wa ukulu yayo yanunghila ni kuichangula myendo kwa machichi yake. Mbale wake Lazalo nde uyo wadali odwala. Chimwecho achalongo wake Lazalo onjhe adatuma uthenga kwa Yesu, "Ambuye mmbwenji lanu wadwala!"
Yesu yapo wadavela chimwecho, wadakamba, "Lazalo siwamwalila kwa utenda uno, nambho wadwala ndande ya kwaapacha Amnungu ulemelelo, wadwala dala Mwana wa Amnungu walemekezedwe kupitila utenda umeneo."
Yesu wadali ni ubwenji wa pamtima ni Masa ni Malia ni Lazalo. Yapo wadavela kuti Lazalo wadwala, Yesu wadaendekela kukhala pamalo pajha wadali kwa masiku yawili. Ndiipo pambuyo pa yameneyo, wadakambila oyaluzidwa wake, "Chipano tiyeni tibwelenjho ku Yudea!"
Oyaluzidwa wake adamkambila, "Oyaluza! Yapita ndhawi yo chepa Ayahudi yapo amafuna kuiiphani kwa myala, ndande yanji mfuna kupitanjho kumeneko?"
Yesu wadayangha, "Bwanji saa za usana osati khumi ni ziwili? Chimwecho mundhu akayenda usana siakhoza kujhikhuwala ndande aliona dangalila la jhiko lino. Nambho usiku mundhu wajhikwala ndande dangalila palibemo mkati mwake." Yesu yapo wadakamba mawu yameneyo, wadaakambila, "Mbwenji lathu Lazalo waghona litulo, nambho ine sinipite kumuucha."
Oyaluzidwa wake adamkaambila, "Ambuye ngati waghona, siwauke."
Anyiiwo amaghaniza wamakamba kuti waghona litulo, nambho wamakambilila nyifa ya Lazalo. Ndiipo, Yesu wadakambila popande kwa bisa, "Lazalo wamwalila,
Domínio sobre a natureza
Jesus acalmou a tempestade, andou sobre as águas e multiplicou pães. A natureza obedece à voz do seu Criador.
Yesu watuliza mwela
Yesu wadakwela mboti, ni oyaluzidwa wake adamchata. Pampajha kudachokela mwela mnyanja, ata mafunde yadayamba kulibula boti. Yesu wadando gona litulo. Oyaluzidwa adamchata, adamuucha nikukamba, "Ambuye, tilamicheni, titobila!"
Yesu wadaayangha, "Imwe wandhu achikulupi chochepa, ndandeyanji muopa?" Yesu wadaima nukutuliza mwela ni nyanja idagona.
Wandhu adadabwa, adajhifunjha, "Mundhu wabwanji uyu? Ata mbhepo ni mafunde vimvela!"
Ujhulo yapo udafika, oyaluzidwa wake adamchata ni kumkambila, "Malo yano ni paphululu, jhuwa litobila. Walole wandhu apite kumijhi akajhigulile chakudya."
Yesu wadaakambila, "Siifunika achoke, anyiimwe mwachinawene wake mwaapache chakudya."
Anyiiwo adamuyangha, "Tulinayo mabumunda isanope ni njhomba ziwili."
Yesu wadaakambila, "Nipelekeleni pano." Wadaakambila wandhu akhale mmaujhu. Yesu wadatenga mabumunda yasano ni njhombha ziwili zijha, wadakweza maso yake kumwamba, wadamyamika Mnungu. Halafu wadabandhula mabumunda ni kwaapacha oyaluzidwa wake, naonjho oyaluzidwa wake wadaagawila wandhu. Wandhu wonjhe adadya ni kukhuta. Oyaluzidwa adakokola vidufya ivo vidakhalila ni kujhaza miseche khumi ni iwili. Wachimuna yawo adadya adali ngati elufu zisano, nambho waachikazi ni wana siadawelengedwe.
Mmalenga kucha, Yesu wadaachata oyaluzidwa uku niwayenda pa mwamba pa majhi.
Yesu waapacha chakudya wandu alufu zinai
Ndiipo Yesu wadaatana oyaluzidwa wake ni kwaakambila, "Nililengela lisungu gulu ili la wandhu, ndande yake akhala ni ine kwa masiku yatatu, ni chipano alibe chakudya icho chakhalila. Ine sinifuna kwaalaila akali ni njala, akhoza kukomoka mnjila."
Oyaluzidwa wake adaafunjha, "Pano tili ni paphululu, bwanji, sitipate kuti chakudya chokhoza kwaakwanila wandhu wonjhewa?"
Yesu wadaafunjha, "Muli ni mabumunda yangati?"
Anyiiwo adayangha, "Mabunda saba ni njhomba zazing’onozing’ono zochepa."
Yesu wadalikambila gulu la wandhu lijha likhale panjhi. Ndiipo wadatenga mabumunda yajha saba ni njhomba zijha, wadamuyamika Mnungu, wadabandula ni kwaapacha oyaluzidwa wake, nawo wadaagawila wajha wandhu. Wandhu wonjhe adadya ni kukhuta. Ndiipo oyaluzidwa wake adakusa vijha vidakhalila nikujhaza miseche saba. Waachimuna yawo adadya adali ngati elufu zinayi, waachikazi ni wana siadawelengedwe.
Kuchocha nsongho mnyumba ya Mnungu
Yesu ni oyaluzidwa wake yapo adafika ku Kapelinaumu, wandhu alandila nsongho wa mnyumba ya Mnungu adamchata Petulo ni kumfunjha, "Bwanji, oyaluza wanu wachocha nsongho wa mnyumba ya Mnungu?"
Petulo wadayangha, "Yetu, wachocha."
Petulo yapo wadalowa mkati, Yesu wadayamba kumfunjha, "Simoni, iwe uona bwanji? Mafumu ajhiko alandila malipilo ni nsongho kuchoka kwa ayani? Kwa wandhu wao kapina kuchokela kwa alendo?"
Petulo wadamuyangha Yesu, "Kuchoka kwa alendo."
Yesu wadamkambila, "Ni bwino, wandhu wao saafunika kuchocha nsongho. Nambho sitifuna kwaakwiicha wandhu anyiyawa, pita kunyanja ukawejhe, utenge njhomba yoyamba kukodwa, uiyasamiche kamwa lake, ni mkati mwake siukomane ndalama. Itenge ukalipile nsongho yaine ni ukajhilipile iwe."
Yesu wauleswa mkuyu
Umawamawa yesu yapo wamabwela kuchokela ku Besaniya kupita kumujhi, wadavela njala. Wadauona mtengo wa mkuyu mbhepete mwanjila, wadaupitila nambho siwadapate chipacho chilichonjhe, udali ni machambape, wadaukambila ujha mtengo, "Usadapachanjho vipacho!" Pampajha mkuyu ujha udauma.
Oyaluzidwa wake yapo adapenya chindhu chijha chidachitika, adadabwa kupunda ni kufunjha, "Ndande yanji mtengo uwu wauma kankamojhi?"
Yesu wadakambila, "Zene nikukambilani, ngati simukhulupilile popande kukayikila, mkhoza kuchita osati ichipe nachita pamtengo, nambho mkhoza kulikambila pili ili, ‘Zuka ukajhitaye mnyanja,’ siikhale chimwecho. Mukakulupilila chindhu chilichonjhe simpembhe mmapembhelo, simulandile."
Papajha mwela waukulu udachokela, ni mafunde yadalibula lijha boti wadalimo Yesu mbaka lidayamba kujhala majhi. Yesu wadali kumbuyo kwa lijha boti wadatogonela philo, oyaluzidwa wake adamuucha ni kumkambila, "Oyaluza, simganizila kuti ife titobila?"
Ndiipo Yesu wadauka ni kuunyindila mwela, "Khala chete!" Pampajha mwela udasiya ni nyanja idagona.
Chimwecho Yesu wadaakambila oyaluzidwa wake, "Ndande yanji muopa? Bwanji, mkali mlibe chikulupililo?"
Oyaluzidwa wake adaopa kupunda, adafunjhana, "Mundhu wa mtundu wanji uyu mbaka mwela umvela?"
Ujhulo yapo udajha, oyaluzidwa adamchata Yesu, adamkambila, "Pamalo pano ni paphululu, ni jhuwa litobila. Waakambile wandhu apite mminda ni mvijhijhi va pafupi akajhigulile chakudya." Nambho Yesu wadaakambila, "Mwachinawene wake mwapache chakudya." Ni anyiiyo adamfunjha, "Bwanji, tipite kugula mabumunda ya dinali miyambili ni kwapacha wandhu adye?" Yesu waadafunjha, "Mli ni mabumunda yangati? Pitani mkapenye, mkaiwelenge." Yapo adawelenga, adamkambila, "Yalipo mabumunda yasano ni njhomba ziwili."
Ndiipo, Yesu wadaakambila oyaluzidwa wake, waakambile wandhu akhale magulu mgulu pamachamba yayawisi. Chimwecho adakhala magulu ya wandhu miya ni ya wandhu amsini. Ndiipo, Yesu wadayatenga yajha mabumunda yasano ni zijha njhomba ziwili, wadapenya kumwamba, wadamuyamika Mnungu, ndiipo wadayadula yajha mabumunda. Wadaapacha oyaluzidwa wake kuti wagawile wandhu. Chinchijha wadagawila wandhu zijha njhomba ziwili. Wandhu wonjhe adadya ni kukhuta. Ndiipo oyaluzidwa wake adatondola vidufya va mabumunda ni njhomba ivo vidakhalila, ni adajhaza miseche khumi ni iwili. Wachimunape yawo adadya yajha mabumunda adali ngati elufu zisano.
Ndiipo, Yesu wadaaona oyaluzidwa wake niavutika kwa kupalasa nghafi, ndande mbhepo imaabula kwa mbhavu. Mmalengakucha, Yesu wadayendela oyaluzidwa wake uku niwayenda pamwamba pa majhi, wamafuna kwapitilila. Yapo adamwona ni wayenda pamwamba pa majhi, amaganizila udali mzilimu, adabula pokhoso. Pakuti wonjhe adamwona, ni adaopa. Yesu wadaakambila, "Jhitileni mtima! Ni ine! Msadaopa!" Ndiipo wadakwela mboti umo adali woyaluzidwa, ni mbhepo idasiya, oyaluzidwa wake adazizwa kupunda,
Yesu waapacha chakudya wandhu elufu zinayi
Pa masiku yameneyo, gulu lalikulu la wandhu lidapezananjho, ni adalibe chakudya. Ndiipo, Yesu wadaatana oyaluzidwa wake, ni kwakambila, "Nialengela lisungu wandhu anyiawa, ndande akhala niine masiku yatatu ni alibe chindhu cha kudya. Nikaasiya abwele mmakhomo yao uku ali ni njala, siakomoke mnjila ndande wina achokela kutali."
Oyaluzidwa wake adamfunjha, "Pano ni paphululu, sitipate kuti chakudya cha kwaapacha wandhu wonjhewa?" Yesu wadaafunjha, "Muli ni mabumunda yangati?" Adamuyangha, "Tili ni mabumunda saba."
Yesu wadaakambila wandhu akhale panjhi. Wadayatenga yajha mabumunda saba, wadamuyamika Mnungu, wadaibandhula ni kwapacha oyaluzidwa wake wagawile wandhu, nawo oyaluzidwa wake adachita chimwecho. Chimwechonjho adali ni njhomba zazing’onozing’ono zochepa. Yesu wadamuyamika Mnungu, ni chinchijha wadaakambila oyaluzidwa wake wagawile wandhu. Wandhu adadya ni kukhuta. Ndiipo woyaluzidwa wake adakusa vakudya vidakhalila ni kujhaza miseche saba. Ni wandhu yawo adadya adali ngati elufu zinayi. Ndiipo Yesu wadaalaila wandhu apite kumakomo yao,
Yesu wauleswa mtengo wa mtini
Umawa wake yapo amachoka ku Besania kupita ku Yelusalemu, Yesu wadali ni njala. Wadauona mtengo wa mtini kwa patali, uwo udali ni machamba yambili. Wadauchata kuti wapenye ngati wakhoza kupheza chipacho chalichonjhe. Nambho yapo wadauwandikila, wadauona ulibe chipacho chalichonjhe, nambho udali ni machamba yokha, pakuti nyengo ya yobala vipacho idali ikali. Yesu wadaukambila ujha mtengo wa mtini, "Kuyambila lelo mbaka muyaya, siubalanjho." Ni oyaluzidwa wake adamvela yapo wadakamba chimwecho.
Yaluzo la mtengo wa mtini uwo udauma
Umawamawa, yapo amapita, adauwona ujha mtengo wa mtini wauma wonjhe. Petulo wadakumbukila icho wadakamba Yesu, wadamkambila, "Oyaluza penyani, ujha mtengo wamtini mdauleswa, wauma"
Yesu wadamkambila, "Mkhulupilileni Mnungu. Nikukambilani uzene, mundhu waliyonjhe wakalikambila phili ili kuti lipite likajivyale mnyanja ya mchele, popande kukhaikila mumtima mwake, nambho wakakhulupilia kuti chindhu icho wachikamba sichichokele, ni Mnungu siwamchitile. Chipano nikukambilani, yapo msali ni kupembha chindhu, khulupililani kuti mwachilandila, nianyiimwe simchipate. Ni yapo mpembhela, mlekelelane, kila mundhu wamlekelele mnjake uyo wamlakwila, ni Atate wanu ali kumwamba siakulekeleleni anyiimwe volakwa vanu.
Yesu wasanghula oyaluzidwa oyamba
Siku limojhi, Yesu wadali waima mbhepete mwa nyanja ya Genesaleti, wandhu ambili adamzongazonga kuvechela mawu ya Mnungu. Wadaona mabwato yawili mbhepete mwa nyanja, iyo idasiidwa ni alovi yao adachoka kupita kukonja makoka yao. Yesu wadalowa mubwato umojhi uwo udali wa Simoni, wadampembha Simoni kuti wambwanyizile kujhiwe, patali pang’ono ni mbhepete mwa nyanja. Wadayamba kuliyaluza gulu la wandhu uku wakhala mkati mwa ujha bwato. Yapo wadamaliza kuyaluza, wadamkambila Simoni, "Peleka mabwato kujhiwe ni mponye makoka kuti mvuwe njhomba." Simoni wadayangha, "Imwe Ambuye tachita njhito yolemecha usiku wonjhe nisitidapate chilichonjhe. Nambho, pakuti mwakamba, tiliponya khokha." Yapo adaponya makoka yao mmajhi, adapata njhomba zambili mbaka makoka yao yadayamba kung’ambika. Adakolosa achanjao yao adali mbwato wina kuti ajhe kwatangatila. Adafika ni adajhaza njhomba mmabwato yonjhe yawili mbaka mabwato yadali ziwaziwa. Simoni Petulo yapo wadaona nchimwecho, wadagwada panjhi pamaso pa Yesu ni kukamba, "Ambuye chokani pamaso panga, chifuko ine ni mundhu wochimwa!" Pakuti iye ni achanjake adazizwa kupunda pakupata njhomba zochuluka. Chimwecho, Yakobo ni Yohana wana a Zebedayo, anyiiwo adali alovi achanjake a Simoni, adazizwa kupunda. Yesu wadamkambila Simoni Petulo, "Usadaopa, kuyambila lelo siuvuanjho njhomba, siukhale owapeleka wandhu kwa Ambuye." Basi, yapo adachicha mabwato yajha pamtunda, adasiya kila kandhu nikumchata Yesu.
Yesu waunyindila mwela kuti usiye
Siku limojhi Yesu wadakambila oyaluzidwa wake, "Tiyeni tiyomboke kuchija kwa nyanja." Chimwecho, adakwela bwato ni kuyamba kuyomboka. Yapo adali mbwato, Yesu wadali ni litulo, wadagona. Mwela waukulu udayamba kuvunduka, ni majhi yadayamba kulowa mu bwato, ni anyiiwo adali pafupi kubila. Woyaluzidwa wake adamchata Yesu ni kumuucha, naakamba, "Ambuye, Ambuye! Tilipafupi kubila!" Iye wadauka ni kuunyindila mwela ni mbhepo, ni mwela udasiya ni kudali mtendele. Ndiipo Yesu wadafunjhaa oyaluzidwa wake, "Chikulupililo chanu chilikuti?"
Nambho anyiiwo adazizwa ni adagwilidwa ni mandha, ni kuyamba kufunjhana, "Uyu ni yani, mbaka wanyindila mwela ni mbhepo ni vonjhe vimvela."
Yesu waunyindila mwela kuti usiye
Siku limojhi Yesu wadakambila oyaluzidwa wake, "Tiyeni tiyomboke kuchija kwa nyanja." Chimwecho, adakwela bwato ni kuyamba kuyomboka. Yapo adali mbwato, Yesu wadali ni litulo, wadagona. Mwela waukulu udayamba kuvunduka, ni majhi yadayamba kulowa mu bwato, ni anyiiwo adali pafupi kubila. Woyaluzidwa wake adamchata Yesu ni kumuucha, naakamba, "Ambuye, Ambuye! Tilipafupi kubila!" Iye wadauka ni kuunyindila mwela ni mbhepo, ni mwela udasiya ni kudali mtendele. Ndiipo Yesu wadafunjhaa oyaluzidwa wake, "Chikulupililo chanu chilikuti?"
Nambho anyiiwo adazizwa ni adagwilidwa ni mandha, ni kuyamba kufunjhana, "Uyu ni yani, mbaka wanyindila mwela ni mbhepo ni vonjhe vimvela."
Yesu wamlamicha mundhu wa viwanda ku Gelasi
Ndiipo, Yesu pamojhi ni oyaluzidwa wake adayomboka nyanja ya galilaya ni kufika kuchijya la jhiko la Agelasi.
Ujhulo, atumwi khumi ni awili wajha adafika kwa Yesu ni kumkambila, "Alaileni wandhu yawa apite kumijhi ni kuminda ili pafupi uko akhoza kupata chakudya ni malo yogona, pakuti pano tili ni paphululu." Nambho Yesu wadayangha, "Anyiimwe nde mwapache chakudya." Anyiiwo adayangha ni kumkambila, "Tili ni mabumunda yasano ni njhomba ziwilipe. Pina tipite tikaagulile chakudya chokwana wandhu wonjhewa?" Wandhu yawo adali pajha, adali wachimuna ngati 5,000.
Ndiipo, Yesu wadakambila atumwi wake, "Akambileni wandhu akhale panjhi mmagulu ya wandhu amsiniamsini." Atumwi khumi ni awili wajha adachita ngati umo adakambilidwa, nawonjho adakhazika wandhu wonjhe. Ndiipo, Yesu wadatenga mabumunda yasano ni njhomba ziwili zijha, wadapenya kumwamba, wadamuyamika ni kumtamanda Mnungu, wadaibandhula mabumunda ni kwapacha wajha atumwi wake kuti wagawile wandhu. Wandhu wonjhe adadya ni kukhuta. Ni atumwi adakusanya vibandhu ivo vidakhala, adavijhaza mu miseche yokwana khumi ni yawili.
Ukwati mmujhi wa Kana
Siku la katatu kudali ni ukwati mmujhi wa Kana, mkoa wa ku Galilaya, nawo amaye wake Yesu adalipo pamwepo, Yesu naye wadalalikidwa pa ukwati pamojhi ni oyaluzidwa wake. Divai yapo idatha, amaye wake adamkambila Yesu, "Divai yatha."
Ndiipo Yesu wadayangha amaye wake, "Ndandeyanji munikambila nghani imeneyo. Ndhawi yochita njhito yanga ikali yosafika."
Chimwecho amake adazikambila mbowa, "Chilichonjhe icho siwakukambileni, chitani,"
Pamenepo padali ni mapipa sita ya myala, iyo yaikidwa kwa chikhalidwe chakusamba cha Chiyahudi, kila mchuko udakakhoza kutenga michuko ya wili kapina itatu ya majhi. Ndiipo Yesu wadaakambila, "Jhazani majhi mmapipa." Ndiipo wadaakambilanjho, "Chipano tungani mkampelekele wamkulu wa phwando." Wamkulu waphwando yapo wadalawa majhi yameneyo, wadapeza yang’anamuka kukhala divai. Siwada jhiwe uko ya choka, nambho anyiyawo adatunga majhi adajhiwa. Wamkulu wa phwando wadamtana wammuna wa ukwati, wadamkambila, "Kila mudhu wayamba kwapacha wandhu divai ya bwino uti, ni akathokumwa ni kukwana, wakonja ijha yosakome. Nambho iwe wachocha divai ya bwino mbaka saino."
Yesu wadachita chizindikilo ichi choyamba ku Kana, ya ku Galilaya wadaalangiza ulemelelo wake, ni oyaluzidwa wake adamkhulupilila.
Yesu wadakamba chimwecho kwa kumuyesa Filipo, pakuti wadajhiwa icho siwachichite.
Ndiipo Filipo wadamuyangha, "Ata ngati tidakhala ni ndalama zochuluka sizikwana kughula chakudya cha kwakwana wandhu anyiyawa, hata ngati kila mmojhi wasiwapachidwe chibandu chaching’onope"
Oyaluzidwa wake mwina uyo wamatanidwa Andulea, mbale wake wa Simoni Petulo, wadamkambila, "Walipo mnyamata mmojhi uyo wali ni mabumunda yasano iyo yakonjedwa kwa ufa wa shayili ni njhomba ziwili, nambho vindhu ivi sivikwana kwa wandhu onjhewa?"
Ndiipo Yesu wadakamba, "Akambileni wandhu akhale panjhi." Pamalopo padali ni matengo yayafupiyafupi yambili. Ndiipo adakhala, adalipo wachimuna elufu zisano. Chimwecho Yesu wadatenga mabumunda, wadaayamika Amnungu, wadagaawila wandhu anyiyao adakhala panjhi, kila mmojhi wadapata ngati umo wadafunila, wadachita chimwecho ni zijha njhomba. Wandhu yapo adakhuta, Yesu wadaakambila oyaluzidwa wake, "Kusani vipande ivo va khala visadataika." Chimwecho adakusa vipande vijha va mabumunda ni kuvitila mvitundu. Adavijhaza mvitundu kumi ni viwili.
Oyaluzidwa yapo adapita patali ngati meta zitatu kapina zinai, adamuona Yesu ni waenda pamwamba pa majhi, wadawandikila sitima, adaopa kupunda. Ndiipo Yesu wadakambila, "Simudaopa, ni ine!" Yapo adamkalibisha Yesu mu mbwato, ndhawi imweyo adafika kujhiko ilo amapita.
Yesu waachokela oyaluzidwa saba
Pambuyo pa yameneyo, Yesu wadaachokela oyaluzidwa wake muchijha la nyanja Tibelia. Wadaachokela chimwechi. Simoni Petulo, Tomaso uyo wamatanidwa Mawila, Nasanaeli mundhu wa ku Kana ya Galilaya, wana awili a Zebedayo ni oyaluzidwa wake wina awili, adali onjhe pamojhi.
Simoni Petulo wadaakambila achaanjake, "Nipita kuvuwa njhomba."
Nao adaamkambila, "Tipita taonjhe kuvuwa." Ndiipo adapita, adakwela mbwato, nambho usiku umeneo sadapate kandhu. Malenga kucha, Yesu wadaima mbhepete mwa nyanja, nambho oyaluzidwa sadajhiwe kuti nde Yesu. Ndiipo, Yesu wadaafunjha, "Anyamata wanga, simudapate njhomba yaliyonjhe?"
Adayangha, "Sitidapate kandhu."
Yesu wadaakambila, "Chichani khokha bendeka lakwene la bwato simupate njhomba." Ndiipo adaponya khokha bendeka limwelo nambho adalepela kuguza ndande ya kuchuluka kwa njhomba.
Chimwecho yujha oyaluzidwa wamakondedwa kupunda ni Yesu, wadamkambila Petulo, "Ekee Ambuye!" Simoni Petulo yapo wadavela kuti Ambuye, wadavala njhalu yake, ndande siwadavale njhalu, ni kujhitaya mmajhi. Nambho anyiwajha oyaluzidwa wina yawo adali pamtunda, adajha pa bwato uku niaguza khokha lojhala njhomba, adali ngati utali mita mia kuchoka pamtunda. Yapo adafika pamtunda adapheza moto wa makala wasonghedwa, njhomba niziochedwa ni bumunda. Yesu wadaakambila, "Majhanazoni njhomba zakumojhi izo mwavuwa."
Chimwecho, Simoni Petulo wadakwela mubwato, wadaguza khokha limenelo mbaka kumtunda lidajhala njhomba zazikulu mia imojhi ni hamsi ni zitatu. Atangati njhomba zidachuluka, sizidang’ambe khokha.
Libertações
Jesus expulsou demônios com autoridade. Os espíritos impuros não resistiam à sua palavra e saíam imediatamente.
Yesu wamlamicha mbowa wa mkulu wa loma
Yesu yapo wadalowa ku Kapelinaumu, wamkulu wa gulu la asilikali mmojhi wa kuloma, wadamchata ni wadampembha wamthangatile. Ndiipo wadakamba, "Imwe Ambuye, mbowa wanga wagona kukhomo, wavuwala ni wadwala kupunda."
Yesu wadamkambila, "Sinijhe kumlamicha."
Nambho yujha wamkulu waloma wadamkambila, "Imwe Ambuye, ine sinifunika imwe mulowe mnyumba mwanga, nambho chochani lamulope, ni mbowa wanga siwalame. Pakuti ata ine nichogozedwa ni waakuluakulu wina, nilinawo asikali yao naachogoza. Nimlamula mmojhi, ‘Pita!’ Nayo wapita, ‘Majha!’ Nayo wakujha ni mbowa wanga, ‘Chita chindhu ichi! Nayo wachita.’ "
Yesu yapo wadavela chimwecho, wadazizwa, wadaakambila wandhu wajha adamchata, "Zene nikukambilani, sinidaone mundhu waliyonjhe mujhiko la Izilaeli uyo wali ni chikhulupi ngati ichi. Zenedi nikukambilani, wandhu ambili siajhe kuchokela dela la kumwela ni kumpoto, nawo siakhale papwando pamojhi ni Ibulahimu ni Isaka ni Yakobo pa ufumu wa kumwamba. Nambho wajha amafunika kukhala mu ufumu wa Mnungu saataidwe kubwalo mumdima, uko sikukhale chililo ni kukukuta mano." Ndiipo Yesu wadamkambila yujha wamkulu wa Loma, "Pita kukhomo, ni ikhale ngati umo wakhulupilila."
Ni mbowa wake wadalama saa imweijha.
Yesu walamicha wandhu awili a viwanda
Yesu yapo wadafika kuchijha la nyanja mujhiko la Agadala, wadakomana ni wandhu awili yao amachoka kumainja, azamwa ni chiwanda. Wandhuwo adali owofya kupunda ni padalibe mundhu uyo wamapita mnjila imeneyo. Pampajha adayamba kubula mapokoso, "Ufuna chiyani kwaife, iwe Mwana wa Mnungu? Bwanji, wajha kutivuticha ndhawi ikali yosakwanila?"
Pafupi ni malo yameyo padali nguluwe zambili zidali kudyela. Ndiipo viwanda vidampembha Yesu, "Ngati utichocha tuloleze tikazilowe nguluwe zijha."
Yesu wadavikambila, "Haya pitani." Pamwepo lijha gulu la viwanda lidaachoka wandhu, lidalowa kwa nguluwe, ni gulu lonjhe la nguluwe lidachika pamchikililo nikufela mmajhi.
Wandhu owesa nguluwe wajha adathawa, adapita kumujhi. Kumeneko adakambilila nghani zijha zidaachokela wajha adazamwa ni viwanda. Ndiipo, wandhu wonjhe adapita kukomana ni Yesu, adampembha kupunda wachoke mujhiko lao.
Yesu wamlamicha uyo siwakhoza kukamba
Wandhu yapo amabwela kwao, wandhu wina adampelekela Yesu mundhu uyo simakhoze kukamba ndande wadali ni chiwanda. Pampajha chiwanda yapo chidachochedwa, mundhu yujha siwamakhoze kukamba wadayamba kukamba. Wandhu adadabwa ni kukamba, "Sichidaonekepo chindhu ngati ichi sichidachokelepo mujhiko la Izilaeli."
Yesu ni Belizebuli
Ndiipo wandhu adampelekela Yesu mundhu osapenya ni uyo siwakhoza kukamba, ndande wadazamwa ni chiwanda. Yesu wadamlamicha, wadakhoza kukamba ni kupenya.
Chikhulupi cha wamkazi
Yesu wadachoka malo yameneyo ni kupita kumijhi ya Tilo ni Sidoni. Wamkazi mmojhi uyo wamakhala mmalo yameneyo, uyo siwadali Myahudi, wadamchata Yesu uku niwalila, niwakamba, "Nilengele lisungu iwe Mwana wa Daudi, mwali wanga wazamwa ni viwanda, wavutika kupunda."
Nambho Yesu siwadamuyanghe mau lililonjhe. Chimwecho oyaluzidwa wake adamchata ni kumpembha kupunda, "Mkambile wachoke ndandeyake watichata uku niwatibulila phokoso."
Yesu wadaayangha, "Ine natumidwa kwa wandhu ajhiko la Izilaeli yawo ali ngati mbelelepe izo zataika."
Wamkazi yujha wadajha ni kumgwadila Yesu, niwapembha, "Pepani Ambuye mnithangatile."
Yesu wadayangha, "Osati bwino kutenga chakudya cha wana ni kwaaponyela agalu."
Wamkazi yujha wadayangha, "Yetu Ambuye, nambho ata agalu akudya vakudya ivo vikugwa panjhi mbuye wake yapo wakudya."
Ndiipo Yesu wadamuyangha, "Wamkazi iwe, chikhulupi chako chachikulu, siuchitilidwe icho udachipembha." Pampajha mwali wake wadalama.
Yesu wamlamicha mnyamata wachiwanda
Yapo adafika pa gulu la wandhu, mundhuu mmojhi wadamchata Yesu, wadamgwadila, wadamkambila, "Ambuye mnilengele lisungu, mwanawanga wali ni njilinjili, ni wavutika kupunda. Ndhawi zambili wagwela pamoto kapina mmajhi. Nidampeleka kwa oyaluzidwa wako nambho siadakhoze kumlamicha."
Yesu wadaayangha, "Imwe mbadwa wopande chikhulupi ni olakwa! Sinikhale ni anyiimwe mbaka liti? Sinikulimbileni mtima mbaka liti? Jhinayoni pano mnyamatayo." Ndiipo Yesu wadachinyindila chiwanda, nacho chidamchoka mnyamata, ni wadalama pampajha.
Pampajha wadatulukila mundhu wachiwanda mujha mnyumba yokomanilana Ayahudi, wadakweza mvekelo waukulu, "Ufuna kutichita chiyani iwe Yesu wa ku Nazaleti? Bwanji, wajha kutipha? Ine nijhiwa kuti iwe ni Woyela, kuchokela kwa Mnungu!" Yesu wadachinyindila chiwanda, "Khala chete! Mchoke mundhu uyu." Chiwanda chimenecho chidamtingiza kwa mbhavu mundhu yujha, chidalila kwa mvekelo waukulu, ni kumchoka.
Yesu wamlamicha mundhu wa viwanda vambili
Yesu ni oyaluzidwa wake adafika kuchijya kwa nyanja ya Galilaya mjhiko la Agelasi. Yesu yapo wadandochikape mboti, wadapezana ni mundhu uyo wadali ni chiwanda, mundhu mmeneyo wamachokela kumainja. Mundhu mmeneyo wamakhala kujha kumainja, ni palibe mundhu wamakhoza kummanga ata kwa maunyolo. Pakuti mala zambili amammanga maunyolo mmanja ni phingu mnywendo, nambho wamadula yajha maunyolo ni kuzidula zijha phingu myendo yake. Wadali ni nghongono zambili, ni padalibe mundhu waliyonjhe wamakoza kumgwila. Usana ni usiku kuzungulila kumainja ni kuphili, niwabula pokoso ni kujhiduladula kwa myala.
Yapo wadamuona Yesu kwa kutali, wadamthamangila, ni kumgwadila. Ni wadakekema kwa mvekelo wa ukulu, "Ufuna kunichita chiyani iwe Yesu Mwana wa Mnungu wali kumwamba kupunda? Nikupembha kwa jhina la Mnungu siudani vuticha!" Wadakamba chimwecho pakuti Yesu wadachikambila, "Chiwanda, choka kwa mundhu uyu"
Ndiipo, Yesu wadachifunjha, "Jhina lako yani"
Wadamuyangha, "Jhina langa ni gulu pakuti tili tambili." Ndiipo adampembha kupunda Yesu wasavitopola vijha viwanda ni kuvipeleka kubwalo kwajhiko lijha. Pafupi ni pamenepo lidalipo gulu lalikulu la nguluwe nilidya pafupi ni phili. Chimwecho vijha viwanda vidampembha Yesu, "Utipeleke kwa nguluwe, utisiye tizilowe izo." Ndiipo Yesu wadavivomeleza, ni vijha viwanda vidamchoka mundhu yujha ni kulowa kwa nguluwe. Gulu lonjhe la nguluwe, zidachikilila kumchikililo ni kubila mmajhi ni kufa, zidali nguluwe alufu ziwili.
Anyiwajha amasunga nguluwe adathamanga, kupita kuvijhijhi ni kuminda kwakambila wandhu yameneyo yadachokela. Wandhu wonjhe adapita kuona yajha yadachokela.
Nambho anyiimwe muyaluza ngati mundhu uyo wali ni chindhu chakwaathangatila atate wake ni amake, nambho mkamba, ‘Thandizo ilo nidakupachani ni Kolobani’ mate yake chindhu ichi chapatulidwa ndande ya kumchochela Mnungu, kwakuyaluza chimwecho mwachekeleza wandhu, siwadathangatila atate wao kapina amao. Chimwecho, ndeumo mulidelela mawu la Mnungu ndande ya makhalidwe yanu yayo mudayalandila. Ni mchita vindhu vambili va mtundu umeneo."
Vindhu ivo vimchita mundhu siwadavomelezeka kwa Mnungu
Yesu wadalitananjho lijha gulu la wandhu, ni kulikambila, "Mnivechele mwaonjhe kuti mjhiwe. Palibe chindhu chilowa mkati mwa mundhu kuchokela kubwalo icho chikhoza kumchita siwadavomelezeka kwa kumlambila Mnungu. Nambho icho chichoka mkati mwa mundhu ndeicho chimchita mundhu siwadavomelezeka kwa kumlambila Mnungu.
Chikhulupililo cha wamkazi mmojhi uyo siwadali Muyahudi
Yesu wadachoka pamenepo, nikupita ku mujhi wa Tilo. Kumeneko wadalowa mnyumba imojhi ni siwadafune mundhu wajhiwe, nambho siwadakhoze kujhibisa. Pajha padalipo ni wamkazi mmojhi uyo wadali ni mwali wa chiwanda, yapo wadavela kuti Yesu wali pajha. Wadajha ni kugwada, pachogolo pa myendo ya Yesu. Yapo wadamgwadila wadampembha Yesu wamchoche chiwanda mwali wake, nambho wamkazi mmeneyo wadali osati Muyahudi, uyo wadabadwila ku Foinike mjhiko la Siliya. Yesu wadamkambila, "Asiye wana akhute uti. Pakuti osati bwino kutenga chakudya cha wana ni kwaponyela agalu."
Nambho yujha wamkazi wadamyangha, "Ambuye ni chazene icho mwakamba, nambho ata agalu ali panjhi pa meza akudya vakudya ivo vikhalila kwa wana."
Yesu wadamkambila wamkazi yujha, "Ndande wayangha bwino, pita kukhomo kwako ni siumpheze mwali wako walama ni chiwanda chamchoka!"
Chimwecho wamkazi yujha wadapita kukhomo lake, wadampheza mwana wake wagona pachika, ni chiwanda chathomchoka.
Mundhu mmojhi kuchokela mgulu la wandhu, wadamuyangha Yesu, "Oyaluza, nakupelekelani mwana wanga kwanu, wali ni chiwanda icho chamchita wakhale bubu. Ndhawi yaliyonjhe yapo chimzamwa chimtaya panjhi ni kumchita wachoke ni matovu mkamwa, ni kutafuna mano yake, ni watouma thupi lake. Nidaapembha oyaluzidwa wako amchoche chiwanda chimenecho, nambho siadakhoze."
Yesu wadaakambila, "Anyiimwe mbadwa ulibe chikhulupililo, sinikhale ni anyiimwe mbaka siku liti? Sinikulimbileni mtima mbaka siku lanji? Majhanayoni pano mwana mmeneyo." Chimwecho adampeleka kwa Yesu yujha wadali ni chiwanda.
Pampajha, chijha chiwanda yapo chidamwona Yesu, chidamchita wakhale ni njili, wadangwa panjhi, wadawalauka ni kuchocha matovu mkamwa. Yesu wadamfunjha tate wayujha mwana, "Bwanji, utenda uwu wampata kuyambila siku lanji?" wadamuyangha, "Kuyambila yapo wadali mwana. Ninyengo za mbili chiwanda chimenecho chimgwecha pamoto ni pamajhi, kuti chimphe. Nambho, ngati mkhoza kuchita chindhu, tilengele lisungu, utithangatile!" Yesu wadamkambila, "Ngati uli ni chikhulupililo, yonjhe yakhozeka kwa uyo wakhulupilila." Pampajha, tate wa yujha mwana wadalila kwa mvekelo, "Nikhulupilila! Nambho chikhulupililo changa chaching’ono, nithangatileni kuti nikhoze kukhulupilila."
Yesu yapo wadaona gulu la wandhu lichuluka kwa chisanga, wadachinyindila chijha chiwanda, "Iwe chiwanda umchita uyu mundhu kukhala wosakamba ni wosavela, nikulamula mchoke mnyamata uyu ni siudamlowanjho!" Pampajha, chijha chiwanda chidatutuma ni kumgwecha njili ni kumchoka. Mwana yujha wadaoneka ngati wamwalila, ni wandhu ambili adakamba, "Wathomwalila!" Nambho Yesu wadamgwila jhanja mnyamata yujha, wadamthangatila kunyakuka, nayo wadanyakuka.
Yesu waalamicha wandhu ambili
Yesu wadachoka mnyumba yokomana Ayahudi ni kupita ku kukhomo kwa Simoni. Apongozi wake wakazi a Simoni amadwala matenda yayakulu kupunda, nianyiiwo adampembha Yesu wamulamiche maeyo. Iye Yesu wampitila mae yujha wadamkwatamila wamkazi yujha ni kuulamula utenda kuti umusiye, ni ujha utenda udamsiya. Ndhawi imweyo wadauka ni kuyamba kwatumikila alendo.
Yapo wamachika mbwato, wadampeza mundhu mmojhi wa mujhi ujha uyo wadali ni viwanda. Mundhu mmeneyo masiku yonjhe siwavale njhalu siwamakale kukhomo wamakhala mmbhanga zozikila wandhu. Yapo wadamuona Yesu, wadalila kwa mvekelo waukulu ni kujiponya panjhi pachogolo pa Yesu ni kukamba kwa mvekelo waukulu, "Iwe Yesu mwana wa Mnungu uli kumwamba kupunda ufuna kunichita chiyani? Nikupembha siudanivuticha!" Pakuti Yesu wachilamula chijha chiwanda chimchoke mundhu yujha. Nyengo zambili chiwanda chijha chimatomchaucha nyengo zambili, wandhu amamchekela mnyumba ni kummanga minyolo mmyendo ni pingu mmanjha ni kumlonda. Nambho wamadula minyololo imeneyo ni pingu ni chiwanda chimenecho chimampeleka kupululu. Yesu wadamfunjha, "Jhina lako yani?" Iye wadayangha, "Ife tili ambili." Iye wadayangha chimwecho ndandeyake wadali ni viwanda vochuluka. Viwanda vimenevo vidampembha Yesu kwa mbili kuti siwadayalamula yapite kujhenje lalikulu.
Padali ni gulu lalikulu la nguluwe pafupi nianyiiwo ilo limadyela mphepete mwa phili. Viwanda vijha vidampembha Yesu kwambili kuti waviloleze vilowe mnguluwezo, ni Yesu wadaviloleza vilowe mnguluwe. Viwanda vicha vidamchoka mundhu yujha ni kulowa mu nguluwe, ni gulu lonjhe la nguluwe lidachikilila kumunjhi ni kubila mnyanja ni kufa.
Wajha owesa yapo adaona yayo yadachokela adathawa, adapita kwakambila wandhu nghani izi mmijhi mwao ni mminda. Wandhu adachoka kupita kuona yayo yadachokela. Yapo adafika yapo wadali Yesu, adamkomana mudhu uyo wadachochedwa viwanda, wakhala pafupi ni myendo ya Yesu, wavala njhalu ni wali ni njelu zake bwinobwino, wandhu wajha adaopa.
Zenedi nikukambilani, pali wina ali pano, siafa akali osauona Ufumu wa Mnungu."
Yesu wang’anamuka nghope
Pambuyo pa masiku nane yapo wadamaliza kukamba yameneyo, Yesu wadaatenga Petulo, ni Yohana ni Yakobo, wadakwelanao kuphili kupembhela. Yapo wamapembhela, maonekedwe ya nghope yake yadang’anamuka, vovala vake vidali voyela ni kung’azikila kupunda. Mwachizulumukila, adaonekana wandhu awili niakamba nayo, wandhu achamenewo adali Musa ni Eliya, yawo adaonekana ali muulemelelo, yawo amakamba ni Yesu kuusu nyifa yake iyo siichokele ku Yelusalemu.
Petulo ni achanjake adagona litulo lalikulu, nambho yapo adathouka, adaona ulemelelo wa Yesu ni wandhu awili yawo adaima pamojhi ni iye. Basi, wandhu awili wajha yapo amasiyana ni Yesu, Petulo wadamkambila Yesu, "Bwana, siikhale bwino ngati sitikhale pamojhi! Basi, timange visakasa vitatu, chimojhi chanu, chinjake cha Musa ni china cha Eliya." Nambho Petulo siwamajhiwe icho wamachikamba.
Yapa, mundhu mmojhi pagulu pajha wadakweza mvekelo, niwakamba, "Woyaluza, majhani mumuone mwana wanga wayokha! Ndande chiwanda chimlowa, nikumchita kuti wabule pokoso ni kumchita ngati wanjilinjili, ni kumchoka matovu mkamwa. Chiwandacho kumvuticha chipunda ni sichifuna kumusiya mwachisanga. Nidapembha oyaluzidwa wako kuti achichoche chiwandacho, nambho alepela." Yesu wadayangha, "Anyiimwe ni mbadwa woipa ni wopande chikhulupililo, sinikhale na anyiimwe kwa ndhawi yaitali yanji kuti munikhulupilile?" Ndiipo Yesu wadamkambila mudhu yujha, "Majhanayo mwana wako pano." Ata yapo mwana yujha wamajha kwa Yesu, chiwanda chidamgwecha panjhi, ni kumbula njilinjili. Nambho Yesu wadachinyindila chiwanda ni kuti chimchoke, wadamlamicha mwana yujha, ni kumbweza kwa atate wake. Wandhu wonjhe adazizwa kupunda kwa ukulu wa Mnungu.
Yesu walosanjho kuusu nyifa yake
Yapo wandhu wajha adali akali kudabwa kuusu yonjhe yajha yadachitika, Yesu wadakambila oyaluzidwa wake,
Yesu ni Belizabuli
Siku limojhi Yesu wamatochocha chiwanda chidamchita mundhu mmojhi kukala bubu. Basi, chiwanda yapo chidamchoka yujha mundhu wadali bubu wadayamba, ni gulu la wandhu lidazizwa.
Ni mmojhi wao wadamdula mbowa wa wamkulu wa ajhukulu khutu lake lakwene kwa upanga. Nambho Yesu wadakamba, "Lekani ikwana!" Nayo wadaligafya khutu la mundhu yujha ni kumlamicha.
Anyiwajha wandhu adatumidwa ni Yohana yapo adachoka, Yesu wadayamba kulikambila gulu la wandhu nghani za Yohana, niwakamba, "Bwanji, yapo mudapita kumuona Yohana kuphululu kujha, mudakhulupilila kuona chiyani? Bwanji, mdapita kuona bango nilitingizidwa ni mbhepo? Bwanji, mudapita kuona chiyani? Bwanji, dapita kumuona mundhu uyo wavala njhalu za mtengo waukulu? Notho! Anyiyawo avala njhalu ngati zimenezo, nikudyelela umoyo waufulu, akhala mnyumba ya mafumu, sakhala mthengo! Nambho, mudapita kuona chiyani? Bwanji, mudapita kumuona mlosi? Yetu, mdapita kumuona mundhu wamkulu kupitilila mlosi. Yohana mmeneyu ndeuyo nghani zake zalembedwa Mmalembo Yoyela,
‘Penya, sinimtume mthenga wanga wakuchogolele,
uyo wakukonjela njila yopita iwe.’ Nikukambilani, pakati pa wandhu wonjhe abalidwa ni wachikazi, palibe uyo wali wamkulu kupitilila Yohana mbatizi. Nambho, uyo wali wamng’ono kwambili pa ufumu wa Mnungu wali wamkulu kupitilila Yohana."
Wandhu wonjhe pamojhi ni wolandila malipilo, anyiyawa adabatizidwa ni Yohana, yapo adavela nghani zimenezo adavomela kuti Mnungu ni wabwino. Nambho a Falisayo ni oyaluza mathauko, adakana yayo adakambilidwa ni Mnungu kuti ayachite, yayo yadakonjedwa ndande yawo, adakana kubatizidwa ni Yohana.