Reino dos céus
O Reino dos Céus é comparado por Jesus a tesouros, sementes e redes. Através de parábolas, Ele revelou os mistérios de um Reino que já está entre nós, mas que se consumará na eternidade.
O valor incomparável do Reino
O Reino dos Céus é como um tesouro escondido ou uma pérola de grande valor. Quem o encontra, vende tudo para possuí-lo.
Chifani cha chindhu cha phindhu lalikulu chabisidwa
"Ufumu wa kumwamba ulingana ni chindhu cha phindu icho chabisidwa mmunda. Mundhu mmojhi wadachivumbula, wadachibisanjho, ni kukondwela kwa kukulu uko wadali nako, wadapita kugulicha vonjhe ivo wadalinavo, ndiipo wadabwela kugula munda ujha."
Chifani cha mwala wa phindhu uwo utanidwa lulu
"Ufumu wa kumwamba ulingana ni wochita malonda mmojhi uyo wamafunafuna lulu ya bwino. Yapo wadapeza lulu imojhi ya phindu lalikulu, wadapita kugulicha vonjhe ivo wadalinacho ni kugula lulu ijha."
Chifani cha mbewu ya ing’ono iyo itanidwa haladali
Yesu wadaakambila chifani china, "Ufumu wa kumwamba ulingana ni mbeu ya ing’ono iyo itanidwa haladali iyo wadatenga mundhu mmojhi, wadaivyala mmunda mwake. Yene niyaying’ono kupunda kupitilila mbeu zonjhe, nambho ikaphuka ikula kupitilila mimela yonjhe. Ikula ni kukhala mtengo, ata mbalame zikujha kumanga visa mndhawi zake."
Chifani cha amila
Yesu wadaakambila chifani china, "Ufumu wa ku Mwamba uli ngati chimwechi, wamkazi mmojhi wadatenga amila, wadaisingizana ni ufa wambili wa ngano, ni wonjhe udatupa."
Parábolas do Reino
Jesus ensinou sobre o Reino mediante parábolas que revelam seu crescimento, seu juízo e a separação final entre justos e injustos.
Chifani cha matengo
Yesu wadaakambila wandhu chifani china, "Ufumu wa kumwamba ulingana ni mundhu uyo wadavyala mbeu zabwino mmunda mwake. Nambho wandhu yapo adagona, mdani wake wadajha, wadavyala matengo pakati pa mapila, nikuchoka. Mapila yapo yadamela ni kuyamba kubala, matengo nayo yadayamba kusetela. Opota njhito adamchata mwene munda, adamkambila, ‘Imwe waakulu, simdavyala mbeu zabwino mmunda mwanu? Chipano matengo yachokela kuti?’ Iye wadayangha, ‘Mdani ndeuyo wachita chimwecho.’ Ndiipo opota njhito wake adamfunjha, ‘Bwanji, ufuna tikayazule?’ Iye wadaayangha, ‘Notho, msadayazula, pakuti pozula matengo, mkhoza kuzulanjho ni mapila. Zisiyeni zonjhe zikulile pamojhi mbaka ndhawi yokolola. Ndhawi imeneyo sinaakambile wokolola kukusa matengo akayamange machakatamachakata ni kuyabucha. Nambho mapila kololani mkaiike mnghokwe mwanga.’"
Yesu wafotokoza mate ya chifani cha matengo
Ndiipo Yesu wadalaila wandhu ni kulowa mnyumba. Oyaluzidwa wake adamchata, adamkambila, "Tikambile mate ya chifani cha matengo yayo yali mmunda."
Yesu wadaakambila, "Mundhu wadavyala mbeu zabwino mmunda, ni Mwana wa Mundhu. Munda ujha nde jhiko, mbeu zabwino zijha nde wandhu wajha ufumu uli wao. Nambho yajha matengo nde wana ayujha Woipa. Mdani uyo wadavyala matengo nde Satana. Vokolola nde kutha kwa jhiko lapanjhi, ni wokolola ni atumiki a kumwamba Amnungu. Ngati mujha matengo yakusidwa ni kubuchidwa moto, nde umo siyakhalilile mathelo ya jhiko. Mwana wa Mundhu siwaatume atumiki wake akumwamba akokole wandhu wajha waachiticha wandhu achite machimo, ni wandhu wonjhe yawo achita voipa, ni siwaaponye kumoto wa muyaya, uko sikukhale kulila ni kukukuta mano. Ndiipo wandhu abwino siawale ngati jhuwa mu Ufumu wa Atate wawo. Uyo wali ni makutu yovela wavele!"
Chifani cha khokha
"Chimchijha, ufumu wa kumwamba ulingana ni khokha ilo liponyedwa mnyanja ni kuvuwa njhomba za mitundu yosiyanasiyani. Khoka yapo lidajhala njhomba zambili, alovi adakokela khokha kumtunda, adakhala panjhi ni kusanghula njhomba, zabwino aziika mngwangu, nambho njhomba zoyipa adazitaya. Kumathelo kwa jhiko sikukhalile chimwechi, atumiki aku mwamba Amnungu siajhe nikwaapatula wandhu oyipa pakati pa wandhu abwino, ni wandhu oyipa saponyedwe kumoto woofya wa muyaya, uko sikukhale kulila ni kukukuta mano."
Quem herda o Reino
Os humildes, os pobres de espírito e as crianças são herdeiros do Reino. Mas é difícil para os ricos entrarem nele.
Chikondwelo cha zene
"Ali ni mwawi wajha ajhiwa kuti amfuna Mnungu
pakuti ufumu wa kumwamba ni wao."
"Ali ni mwawi yao ali ni chisoni
pakuti siathilidwe mtima."
"Ali ni mwawi yao ajhichicha
pakuti Mnungu siwapache jhiko likhale lao."
"Ali ni mwawi yao afuna kupunda kuchita ivo vimkwadilicha Mnungu
ndande Mnungu siwatangatile kuchita chimwecho."
"Ali ni mwawi wajha alengela wina lisungu
pakuti Mnungu siwalengele lisungu."
"Ali ni mwawi yao ali ni mtima wabwino
pakuti saamuone Mnungu."
"Ali ni mwawi wajha apeleka mtendele
pakuti siatanidwe wana a Mnungu."
"Ali ni mwayi anyiyao avutichidwa ndande ya kuchita yayo wafuna Mnungu
Pakuti ufumu wa kumwamba ni wao!"
"Muli ni mwawi wandhu yapo sakutukwaneni ni kukuvutichani ni kukunamizilani voipa ndande yanga. Kondwani ni lulutilani pakuti chikho chanu chachikulu chaikidwa kumwamba. Mchimwecho nde umo adaavuticha alosi akhale anyiimwe mkali wosabdwa."
Yani waliwamkulu pa Ufumu wa Mnungu
Ndhawi imeneyo oyaluzidwa adamchata Yesu, adaamfunjha, "Yani uyo wali wamkulu kupitilila wonjhe mu Ufumu wa kumwamba?"
Yesu wadamtana mwana wamng’ono ni kumwimika pakati pao, Ndiipo wadaakambila, "Zene nikukambilani, ngati simng’anamuka ni kulingana ni wana waang’onoang’ono, simulowa mu Ufumu wa kumwamba. Waliyonjhe uyo wajhichepecha ngati mwana uyu, nde uyo siwakhale wamkulu mu Ufumu wa kumwamba.
Yesu wadaakambila, "Alekeni wana waang’onoang’ono ajhe kwaine, msachekeleza, pakuti Ufumu wa kumwamba ni wa wandhu ali ngati wanawa."
Pamenepo Yesu wadaakambila oyaluzidwa wake, "Zene nikukambilani, siikhale kolimba kwa mundhu wopata kulowa mu Ufumu wa kumwamba. Nikukambilaninjho, ikhozeka chinyama icho chitanidwa ngamila kupyola pa ndhoolo kasindano kusiyana ni mundhu wopata kulowa mu Ufumu wa Mnungu."
Oyaluza wake yapo adavela chimwecho adadabwa, adamfunjha, "Chipano ni yani uyo wakhoza kuomboledwa?"
Yesu wadaapenyecha ni wadakambila, "Vindhu ivi kwa mundhu sivikhozekana, nambho kwa Mnungu vindhu vonjhe vikhozeka."
Buscar o Reino acima de tudo
Jesus ensinou que devemos buscar primeiro o Reino e sua justiça. Nem todo que diz 'Senhor, Senhor' entrará — só quem faz a vontade do Pai.
Sinikujhiwani anyiimwe
"Osati kila uyo wanitana, ‘Ambuye, Ambuye,’ siwalowe muufumu wa kumwamba, nambho niwajhape achita vijha afuna Atate wanga ali kumwamba.
Waliyonjhe uyo siwachata thauko laling’ono kuchokela mthauko ili nikwaayaluza wina kuti achite chimwecho. Mmeneyo siwakhale womng’ono kupunda mu ufumu wa kumwamba. Nambho yujha wachata thauko ni kwaayaluza wina, mmeneyo siwakhale wamkulu mu ufumu wa kumwamba. Zene nikukambilani ngati simuchita umo wafunila Mnungu kupitilila umo achitila Afalisayo ni oyaluza a thauko simulowa mu ufumu wa kumwamba ata pang’ono."
Nambho anyiimwe pembhelani chimwechi,
‘Atate wathu yawo muli kumwamba,
Jhina lanu likwezedwe.
Ufumu wanu ujhe.
Ilo mlifuna lichitike pa jhiko lichitike ngati umo lichitikila kumwamba.
Yohane Mbatizi walalikila wandhu
Pambuyo pa masiku yambili kupita Yohana Mbatizi wadajha ni kuyamba kulalikila wandhu kuphululu la kujhiko la Yudea niwakamba, "Lapani pakuti ufumu wa kumwamba wawandikila!"
Kuchokela nyengo imeneyo Yesu wadayamba kulalikila niwakamba, "Siyani kuchita machimo pakuti ufumu wa kumwamba wawandikila!"
Pitani mkalalikile wandhu Uthenga uwu, ‘Ufumu wa kumwamba wawandikila.’
Zenedi nikukambilani, wandhu ambili siajhe kuchokela dela la kumwela ni kumpoto, nawo siakhale papwando pamojhi ni Ibulahimu ni Isaka ni Yakobo pa ufumu wa kumwamba.
Zene nikukambilani, pakati pa wana wonjhe abalidwa ni wamkazi, siwadachokelepo mundhu wa mkulu kupitilila Yohana Mbatizi. Ata chimwecho, yujha wali wamng’ono kupunda mu ufumu wakumwamba ni wamkulu kupitilila Yohana. Kuyambila masiku ya Yohana Mbatizi yapo wamalalikila mbaka lelo, ufumu wa kumwamba uchuchana kwa mbhavu, ni yawo ali ni mbhavu nde yawo aulanda.
A herança eterna
O Reino dos Céus é inabalável e eterno. Deus nos chama a fazer firme a nossa vocação e eleição para entrar nesse Reino.
Kujhiikila chuma kumwamba
"Msadaopa, anyiimwe muli gulu laling’ono, pakuti Atate wanu akonda kukupachani anyiimwe Ufumu wao.
Mjhiwe kuti wachigololo waliyonjhe, kapina mkazuzu kapina wokhumbila, mundhu ngati mmeneyo siwapata chilinjhonjhe muufumu wa Kilisito ni Mnungu. Mundhu wakhumbilo walambila chiboliboli.