8Chuma cha munthu wolemera chitha kuwombola moyo wake,koma munthu wosauka amamva chidzudzulo.
12Chinthu chochiyembekezera chikalephereka chimalefula mtima,koma chinthu chochilakalaka chikachitikadi chimakhala ngati mtengo wamoyo.
14Malangizo a munthu wanzeru ali ngati kasupe wamoyo;amathandiza munthu kuti asakondwe mu msampha wa imfa.