10 Yehova anayankhulanso ndi Ahazi, 11 "Pempha chizindikiro kwa Yehova Mulungu wako, chikhale chozama ngati manda kapena chachitali ngati mlengalenga."
12 Koma Ahazi anati, "Ine sindipempha; sindikufuna kuyesa Yehova."
13 Apo Yesaya anati, "Imva tsopano, iwe nyumba ya Davide! Kodi sikokwanira kutopetsa anthu? Kodi mudzayeseranso kutopetsa Mulungu wanga? 14 Nʼchifukwa chake Ambuye mwini adzakupatsani chizindikiro: Onani, namwali adzakhala woyembekezera ndipo adzabala mwana wamwamuna, ndipo mwanayo adzamutcha Imanueli.