12 Wagwa pansi bwanji kuchoka kumwamba,
iwe nthanda, mwana wa mʼbandakucha!
Wagwetsedwa pansi pa dziko lapansi,
Iwe amene unagonjetsapo mitundu ya anthu!
13 Mu mtima mwako unkanena kuti,
"Ndidzakwera mpaka kumwamba;
ndidzakhazika mpando wanga waufumu
pamwamba pa nyenyezi za Mulungu;
ndidzakhala pa mpando waufumu pa phiri losonkhanirako,
pamwamba penipeni pa phiri la kumpoto.
14 Ndidzakwera pamwamba pa mitambo;
ndidzafanana ndi Wammwambamwamba."
15 Koma watsitsidwa mʼmanda
pansi penipeni pa dzenje.