13 Pakuti Ine Yehova, ndine Mulungu wako,
amene ndikukugwira dzanja lako lamanja
ndipo ndikuti, usaope;
ndidzakuthandiza.
14 Usachite mantha, iwe Yakobo wofowoka ngati nyongolotsi,
iwe wochepa mphamvu Israeli,
chifukwa Ine ndidzakuthandiza,"
akutero Yehova Mpulumutsi wako, Woyerayo wa Israeli.