Ulemerero wa Ziyoni
1 "Dzuka, wala, pakuti kuwala kwako kwafika,
ndipo ulemerero wa Yehova wakuwalira.
2 Taona, mdima waphimba dziko lapansi
ndipo mdima wandiweyani wagwa pa anthu a mitundu ina,
koma Yehova adzakuwalira iwe,
ndipo ulemerero wake udzaoneka pa iwe.
3 Mitundu ya anthu idzatsata kuwunika kwako
ndipo mafumu adzalondola kunyezimira kwa mʼbandakucha wako.