3 Anthu akufunsa kuti, ‘Chifukwa chiyani ife tasala
kudya pamene Inu simukulabadirapo?
Kodi ife tavutikiranji nʼkudzichepetsa
pamene Inu simunasamalepo?’ "
Yehova akuti, "Komatu tsiku lanu losala kudya, mumachita zinthu zokukondweretsani,
ndipo mumazunza antchito anu onse.
4 Mumati uku mukusala kudya, uku mukukangana ndi kumenyana,
mpaka kumenyana ndi nkhonya zopweteka.
Kusala kudya mukuchitiramu musayembekezere kuti mawu anu amveka kumwamba.
5 Kodi kusala kudya kumene ndimakufuna Ine nʼkumeneku,
kungokhala tsiku loti munthu adzichepetse basi?
Kodi ndi tsiku loti munthu angowerama pansi ngati bango
ndi kumayala ziguduli nʼkuthirapo phulusa nʼkugonapo?
Kodi ndiye mumati kusala kudya kumeneko,
tsiku lokondweretsa Yehova?
6 "Kodi si uku kusala kudya kumene Ine ndimakufuna:
Kumasula maunyolo ozunzizira anthu
ndi kumasula zingwe za goli,
kupereka ufulu kwa oponderezedwa
ndi kuphwanya goli lililonse?