Kuchoka kunyifa kulowa ku umoyo
1 Anyiimwe mudafa ndande ya volakwa ni machimo yanu. 2 Nyengo zijha mmakhala kwa kuchata mtundu wa jhiko lino, ni kumvela mfumu wa chiwanda cha mbhavu ya mlengalenga, chiwanda chalaamulila wandhu yawo chipano samvela Mnungu. 3 Ife nafe taonjhe timakhala ngati anyiiwo, timachata makhumbilo yathu ya jhiko ni kuchita ivo vikwadilicha matupi ni njelu zathu. Nafe mmayambo tidali ngati anyiiwo, timafunika tilangidwe ni Amnungu.
4 Nambho Mnungu ni alisungu kupunda. Adatikonda kwa chikondi chachikulu, 5 ata ngati tidamwalila ndande ya machimo, adatichita amoyo pamojhi ni Kilisito. Kwa ubwino wa Mnungu anyiimwe mwaomboledwa.