3 Ife nafe taonjhe timakhala ngati anyiiwo, timachata makhumbilo yathu ya jhiko ni kuchita ivo vikwadilicha matupi ni njelu zathu. Nafe mmayambo tidali ngati anyiiwo, timafunika tilangidwe ni Amnungu.
4 Nambho Mnungu ni alisungu kupunda. Adatikonda kwa chikondi chachikulu, 5 ata ngati tidamwalila ndande ya machimo, adatichita amoyo pamojhi ni Kilisito. Kwa ubwino wa Mnungu anyiimwe mwaomboledwa.