13 Pakuti anyiimwe mdatanidwa ni Mnungu dala mkale afulu, ufulu wanu usidakhala ndande yochata makumbilo ya thupi, nambho mfunika mtumikilane kwa chikondi. 14 Pakuti thauko lonjhe likwanilichidwa kwa lamulo lino limojhi, "mkonde wa pafupi wako ngati umo ujhikondela wamwene."