Pular para o conteúdo
Publicidade

Aloma 12:1-3

NTNYBL2025 Nyanja

Ukhalo wa kumtumikila Mnungu

1 Chipano, achabale wanga, pakuti Mnungu ni walisungu kupunda, nikupembhani kwa mtima wanga wonjhe, mjhichoche mwachinawene kwa Amnungu mkhale ngati njhembe yo pyeleza iyo ili yamoyo, iyo ili ya Mnungu mwene ni yomkwadilicha Mnungu. Iyi nde njila yanu ya zene yakumlambila Mnungu. 2 Simudaganizila ngati wandhu ajhiko lino umo aganizila, nambho Mnungu siwakung’anamuleni maganizo yanu kwa kuganizila bwino. Pamenepo ndipo simkhoze kujhiwa icho wafuna Mnungu ni kujhiwa chindhu chili cha bwino, ilo limkwadilicha ni kuchita ngati umo ifunikila.

3 Kuchokana ni ubwino uwo wanipacha Mnungu, nikukambilani anyiimwe mwaonjhe, simdajhiona kuti anyiimwe ni abwino kusiyana ni umo mmafunika kukhala. Mjhipime mwachinawene umo muli kwa chipimo cha chikhulupi icho Mnungu wamgawila kila mmojhi,

Em outras traduções

  1. TCCL Abra a Palavra de Deus em Chichewa Contemporâneo

    1 Nʼchifukwa chake ine ndikukupemphani abale, mwa chifundo cha Mulungu, kuti mupereke matupi anu monga nsembe yamoyo, yopatulika ndi yokondweretsa Mulungu. Nsembeyi ndiye kupembedza kwanu kwa uzimu. 2 Musafanizidwenso ndi makhalidwe a dziko lino koma musandulike pokonzanso maganizo anu. Ndipo mudzadziwa ndi kuzindikira chifuniro chabwino cha Mulungu chomwe ndi chokondweretsa ndi changwiro.

    3 Chifukwa cha chisomo chopatsidwa kwa ine, ndinena kwa aliyense wa inu kuti musadziyenereze nokha kuposa mmene mulili. Koma mudziganizire nokha modzichepetsa, molingana ndi muyeso wa chikhulupiriro chimene Mulungu wakupatsani.

Direitos das traduções citadas

Estes versículos te tocaram? Ore agora!

+581 estão orando agora.

Junte-se à corrente de oração.