4 Nambho ndhawi yeneyene yapo idakwana Amnungu adamtuma Mwana wao uyo pajhiko lino la panjhi. Mwana uyo wadabadwa ni wamkazi, mwana mmeneyo wadachgozedwa ni thauko la Musa, 5 waombole anyiwajha achogozedwa ni thauko, dala ife Ayahudi tichitidwe kukhala wana Amnungu.
6 Ndande chipano anyiimwe ni wanawake, Amnungu wautuma mzimu wa mwanawake mmitima mwanu, mzimu uwo utichita kuti timtane Mnungu, "Atate wathu."