Pular para o conteúdo
Publicidade

2 Coríntios 9:6-11

NTNYBL2025 Nyanja

6 Zindikilani mau yaya, uyo wavyala pang’ono wakolola pang’ono, uyo wavyala zambili wakolola zambili. 7 Kila mmojhi, chipano wachoche ngati umo wakhozela, kwa mtima asati kuchocha kwa kudandaula kapina kukakamizidwa, pakuti Mnungu wamkonda yujha wachocha kwa mtima kokondwela. 8 Mnungu wakhoza kukupachani anyiimwe kupitilila yayo muyafuna, dala mkhale ni kila chindhu icho muchifuna siku zonjhe, dala mpunde kuthangatila kwa kila njhito iyo ili yabwino. 9 Ngati umo yalembedwa mmalembo ya Mnungu,

"Iye wachocha kwa ubwino,

wapacha osauka,

ubwino wake ulama muyaya."

10 Mnungu uyo wampacha mlimi mbeu ndande yovyala niuyo wampacha chakudya, siwakupacheni mbeu izo muzifuna, siwazichite zimele, zikule ni kukupachani vokolola vambili va ubwino wanu. 11 Iye siwakuchiteni kupata kwa kila kandhu, dala kwa ubwino wanu wandhu amuyamike Mnungu, kupitila ife.

Em outras traduções

  1. TCCL Abra a Palavra de Deus em Chichewa Contemporâneo

    6 Takumbukirani mawu awa: Amene adzala pangʼono, adzakololanso pangʼono, ndipo amene adzala zochuluka, adzakololanso zochuluka. 7 Munthu aliyense apereke chimene watsimikiza mu mtima mwake kuti apereka, osati monyinyirika kapena mokakamizidwa, pakuti Mulungu amakonda wopereka mokondwera. 8 Ndipo Mulungu akhoza kukudalitsani kwambiri, kuti inuyo nthawi zonse mukhale ndi zinthu zokukwanirani, ndiponso ndi zina zochuluka kuti muthandize pa ntchito zonse zabwino. 9 Paja analemba kuti,

    "Wopereka mphatso zake mowolowamanja kwa osauka,

    chilungamo chake chimanka mpaka muyaya."

    10 Tsono Mulungu amene amapereka mbewu kwa wofesa, ndiponso chakudya kuti adye, adzaperekanso mbewu mʼnkhokwe zanu ndi kuzichulukitsa. Iye adzachulukitsanso zipatso za chilungamo chanu. 11 Adzakulemeretsani pa zonse kuti mukhale owolowamanja pa nthawi zonse. Ndipo kuwolowamanja kwanu kudzera mwa ife, kudzakhala kuthokoza kwa Mulungu.

Direitos das traduções citadas

Estes versículos te tocaram? Ore agora!

+581 estão orando agora.

Junte-se à corrente de oração.