13 Chimwecho, valani vida ivo wakupachani Mnungu, mkhoze kulimbana pa siku la mavuto, ni mkabulana mbaka pothela simuendekele kukhala nganganga.
14 Chipano, imani nganganga, muli wojhimanga zene ngati lamba muchiuno mwanu, kuvomelezeka kukhale ngati chivalo cho jhikengelela pamtima, 15 mkhale tayali kulalikila Uthenga Wabwino wa mtendele ngati vilato myendo mwanu. 16 Kupitilila yonjhe, chikhulupi chikhale chitetezo mmanja mwanu, chikhoze kizithima misonga ya moto ya satana. 17 Ulandileni uomboli ngati chisoti cha chichulo, ngati upanga wa Mzimu uwo uli mawu la Mnungu. 18 Pembhelani siku zonjhe kwa mbhavu ya Mzimu, nikupembha mthandizo wa Mnungu. Chezelelani popande kulema nimwapembhela wandhu onjhe a Mnungu.