12 Chindhu ichi ni kwa wonjhe, pakuti balibe kusiyana kwa Ayahudi ni anyiawo osati ayahudi, Mbuye wa wonjhe ni mmojhi, naye wali ni ubwino kupunda kwa wandhu ampembha. 13 Yalembedwa chimwechi mmalembo ya Mnungu, "Mundhu waliyonjhe uyo siwapembhe kwa ulamuli wa jhina la Ambuye siwaomboledwe."
14 Chipano sampembhe bwanji iye samkhulupilila? Nianyiiwo, samkhulupilile bwanji ngati sadavela nghani zake? Nisavele bwanji ngati palibe mundhu olalikila? 15 Ni wandhu salalikile bwanji ngati sadapelekedwe? Ngati umo yalembedwa mmalembo ya Mnungu, "Chindhu chokwada kupunda kujha kwa wajha alalikila Uthenga Wabwino!" 16 Nambho asati wonjhe adaulandila Uthenga Wabwino. Nde ndande Isaya wadakamba, "Mbuye ni yani uyo wadakhulupilila uthenga wathu?" 17 Chimwecho, chikhulupi chichokana ni kuvela Uthenga Wabwino, ni uthenga umeneo uchokana ni mawu la Kilisito.