12 Chipano machimo siyadalamulanjho wiwalo va matupi yanu yayo siyafe, ni siyadakuchitani muyavele makumbilo yanu. 13 Msidachichita chiwalo chilichonjhe cha matupi yanu kuhala chindhu cho chitila machimo. Pambuyo pake jhichocheni mwachinawenewake kwa Mnungu ngati wandhu mwa hyuka, vichocheni viwalo vanu kwa Mnungu ngati vindhu ivo vavomelezeka. 14 Machimo siyakulamulilani njhoni, pakuti anyiimwe simchogozedwa ni thauko, nambho mchogozedwa ni ubwino.
Akapolo akuchita yayo yamkwadilicha Mnungu
15 Chipano tikambe chiyani? Tichite machimo ndande sitichogozedwa ni thauko nambho tichochogozwedwa ni ubwino? Notho! 16 Mjhiwa kuti anyiiwe mkajhichocha mwachina wene ngati akapolo wa mundhu waliyonjhe mkhala akapolo azene amundhu yujha, ni ngati mkachichocha kukhla akapolo wa machimo mathelo yake ni nyifa, nambho mkachichocha kumvela Mnungu simkhale ovemelezeka kwa Mnungu? 17 Nambho chipano nimuyamika Mnungu, pakuti anyiimwe kale mdali akapolo amachimo, mwakhala ovela kwa mtima yanu yonjhe kwa mayaluzo mdayaluzidwa. 18 Mdaomboledwa kuchokela kuukapolo wa machimo, chipano mwakhala akapolo akuchita yajha yamkwadilicha Mnungu.