Nghondo mkati mwa mundhu
14 Tijhiwa kuti thauko ni lachizimu, nambho ine osati wa Chizimu, ine naghulichidwa dala nikhale kapolo wa machimo. 15 Sinichijhiwa icho nichichita, pakuti chijha nichifuna sinichichita, nambho icho sinichifuna ndeicho nichichita. 16 Ngati nichita chijha sinichifuna ine kuchita, pamenepo nivomela kuti lijha thauko ni la bwino. 17 Nambo kwa uzene osati inenjho nichita chijha sinichifuna, nambho ni yajha machimo yakhala mkati mwanga nde yayo yanichita nichite icho sinichifuna.