8Kupitilila yameneyo niwelenga vindhu vimenevo sinipata nikailinganicha ni kupata lalikulu lipitilila mwa pakumjhiwa Kilisito Yesu Ambuye wanga. Ndande yake navomela kusiya kila kandhu nayaona yalibe mate ili nimpate Muomboli
9nane nilunjane nayo. Nisidajhi vomela namwene kwa kuchata thauko ila ijha ipezeka kwa chikhulupi mwa Kilisito kuvoleka kuchokela kwa Mnungu kwa chikhulupi.
17Siku limojhi Yesuyapo wamayaluza wandhu, Afalisayo ni oyaluza a mathauko kuchokela kumijhi yonjhe ya Yudea ni Galilaya, ni Yelusalemu adajha pamwepo. Ni mbhamvu za Ambuye zidali ni iye kuti walamiche odwala.
10Chipano mmeneyo uyo wachika nde uyo wadakwela kumwamba kupunda, dala waenele kila pamalo.
16Kwa kuchogozedwa ni Kilisito, thupi lonjhe likalunjidwa ni kugwilizidwa pamojhi, kwa mthandizo wa kila chiwalo. Chipano, kila chiwalo chichita njhito yake, thupi lonjhe likula lene ni kujhikonja muchikondi.
5Mundhu yujha wadaapenya niwalindilila kupata kandhu kuchokela kwa anyiiwo.
21uyo wamafunika kulandilidwa kumwamba mbaka ijhe ndhawi yochita kila kandhu chikhale cha chipano. Nghani izi zimakambidwa ni Mnungu kupitila alosi wake woyela kuyambila chiyambo cha jhiko la panjhi.
23Mundhu waliyonjhe uyo siwamuvela mlosi mmeneyo, siwapatulidwe kuchokela kwa wandhu a Mnungu ni kuphedwa.’
1Chinchijha, Saulo wadakondwelechedwa ni kujha kuphedwa kwa Sitefano.Kuyambila siku lijha wandhu adamkhulupilila Kilisito kujha ku Yelusalemu adayamba kuvutika kupunda. Wandhu wonjhe yawo adamkhulupilila Kilisito, kusiya atumwi, adamwazika ku malo yonjhe ya Yudea ni Samaliya.
3Ndhawi imeneyo Saulo wamatowavuticha wandhu yawo adamkhulupilila Kilisito. Wadapita kila nyumba niwaakwekweta wandhu yawo adamkhulupilila Kilisito, wachikazi ni wachimuna ni kwaaika mundende.
7Viwanda vidaachoka wandhu kwa kukweza mvekelo waukulu, wandhu wopuwala ni wovuwala adalamichidwa.
34Niyani uyo siwalamule kwa kwalanga? Palibe! Pakuti Kilisito nde uyo wadamwalila, ni wadahyuka ni wakhala kumalo ya ulamulilo kwa Mnungu iye watipembhela.
35Niyani wakhoza kutiika patali nichikondi cha Kilisito? Bwanji ni kulaga, kapina mavuto, kapina njala, kapina kutedwa njhalu, kapina kuofyedwa kuphedwa?
39kapina jhiko la kumwamba kapina jhiko la panjhi kupunda. Palibe choumbidwa chalichonjhe chikhoza kutiika patali ni chikondi cha Mnungu mkati mwa Kilisito Yesu mbuye wathu.