Kuvomelezedwa kwa njila ya kukhulupilila
21 Nambho chipano njila ya kwachita wandhu avomelezeke kwa Mnungu ili padanga, popande kukhulupilila thauko, osati ngati umo lidakambila thauko la Musa ni malembo ya alosi a Mnungu vonjhe vikambilila chindhu chimenecho. 22 Mnungu waavomela wandhu kuti ni woyela kwa njila ya chikhulupi chao kwa Yesu Kilisito, Mnungu wachita chimwecho kwa wonjhe akhulupilila, siwapatula Ayahudi ni wandhu yawo osati Ayahudi. 23 Wandhu wonjhe achita machimo, palibe uyo wali wabwino ni wonjhe ataiza kulemekezedwa ni Mnungu. 24 Nambho kwa mbhaso ya ubwino wa Mnungu, wandhu wonjhe avomelezedwa kuti ni abwino pachogolo pa Mnungu kwa njila ya Yesu Kilisito uyo wadaombola.