21 Chipano najhiwa chimwechi, kuti nifuna kuchita chindhu chabwino, nambho nijhipeza kuti chijha chilichoipa nde ichonisangha. 22 Mumtima wanga, nilikondwela thauko la Mnungu. 23 Nambho niona kuti mkati mwanga kuli thauko lina ilo lichita njhito ilo lichuchana ni maganizo yanga ya bwino. Thauko limenelo linichita kukhala kapolo wa thauko la machimo yayo yachita njhito mthupi mwanga.