35 Siku zonjhe nachita njhito ngati chifani kwanu, kulangiza kuti tifunika kwatangatila osauka, uku nitikumbukila mawu ya Ambuye Yesu mwene yayo yakamba, ‘Ali ni mwawi anyiawo achocha kusiyana ni anyiiawo alandila.’"
36 Poolo yapo wadamaliza kukamba chimwechi wadagwada pamojhi ni anyiiwo wonjhe, ndiipo adampembha Mnungu. 37 Wandhu wonjhe adalila ni kumvumbatila Poolo, ndiipo adamlaila. 38 Icho chidaadandaulicha ni yajha mawu wadaakambila Poolo kuti samuonanjho. Ndiipo adampelekeza mbaka ku sitima.