12 Chipano kila mmojhi wathu siwakambe nghani zake mwene pachogholo pa Mnungu.
Usidamlakwicha mbale wako
13 Chipano tisiye kwalamula okhulupilila anjathu, nambho tilamule kuti tisiye kuchita chalichonjhe icho sichimchitiche okhulupilila mnjathu wachite machimo. 14 Pakulunjhana ni Ambuye Yesu, nijhiwa zenedi kuti palibe chindhu chalichonjhe sichivomelezeka pa kumlambila Mnungu, nambho mundhu wakaganiza kuti chindhu chakuti sichivomelezeka pakumlambila Mnungu, chimwecho sichivomelezekadi.