35 Niyani wakhoza kutiika patali nichikondi cha Kilisito? Bwanji ni kulaga, kapina mavuto, kapina njala, kapina kutedwa njhalu, kapina kuofyedwa kuphedwa? 36 Ngati umo malembo ya Mnungu yakambila,
"Ndande yako, tifunidwa ni nyifa usana ni usiku,
tawelengedwa ngati mbelele zopedwa."
37 Nambho pa vindhu vimenevo vonjhe, tikhoza ndande tithangatilidwa ni Klisito uyo watikonda. 38 Pakuti nijhiwa uzene kuti palibe chindhu chikhoza kutipatula ni chikondi cha Mnungu ikhakhala nyifa kapina umoyo, kapina atumiki a akumwamba kapina mbhavu zina za kumwamba, kapina yayo yachokela saino, kapina yayo siyachokele pambuyo, kapina ulamulilo, 39 kapina jhiko la kumwamba kapina jhiko la panjhi kupunda. Palibe choumbidwa chalichonjhe chikhoza kutiika patali ni chikondi cha Mnungu mkati mwa Kilisito Yesu mbuye wathu.