2 Yapo amampembha Mnungu ni kumanga kudya, Mzimu Woyela udaakambila, "Nipatulileni Banaba ni Saulo, kuti achite njhito iyo naatanila kuchita."
3 Yapo adamaliza kumanga kudya ni kupembhela, anyiiwo adaasanjika manja Banaba ni Saulo ni kwasiya ajhipita.
Banaba ni Saulo alalikila Uthenga Wabwino ku Kipulo
4 Banaba ni Saulo yapo adatumidwa ni Mzimu Woyela, adachikilila ku Seleukiya ni kupitanjho mbaka ku chilumba cha Kipulo.