Pular para o conteúdo
Publicidade

Atos 16

10 Poolo yapo wadaona maloso yameneyo, tidakonjeka msanga ni kumanga ulendo wopita kumujhi wa Makedoniya. Tidazindikila kuti Mnungu watitana kuti tikalalikile Uthenga Wabwino kujha ku Makedoniya.

Lidiya wamkhulupila Kilisito

11 Tidamanga ulendo kwa sitima kuchokela ku Tuloa mbaka ku chilumba cha Samosilake. Siku ilo lidachatila tidayendekela ni ulendo mbaka ku mujhi wa Neapoli. 12 Tidachoka kumeneko ni kupita mbaka ku Filipi, mujhi waukulu wa Makedoniya, uwo udali panjhi pa ulamulilo wa Aloma. Tidakhala mmujhi umenewo kwa masiku yochepa. 13 Siku Lopumulila tidapita kubwalo kwa mujhi, mmbhepete mwa mchinje uko timaganiza kuti malo yochitila mapembhelo. Tidakhala ni kuyamba kukamba ni wachikazi yao adasonghana kumeneko. 14 Mmojhi wa anyiwajha adativechela wadali Lidiya uyo wadachokela ku Tiyatila, uyo wamagulicha njhalu za mtengo wa ukulu. Iye wadali mundhu wa bwino. Ambuye Mnungu adamchita Lidiya wakhulupilile chijha wamakamba Poolo. 15 Iye pamojhi ni wandhu wonjhe yawo amakhala mnyumba mwake adabatizidwa. Ndiipo wadatitana kunyumba kwake, niwakamba, "Ngati muuona kuti ine nakhulupilila Ambuye Yesu, majhani kukhomo kwanga mkhale." Wadatipembha kupunda tipite kukhomo lake.

Poolo ni Sila aikidwa mndende

16 Siku limojhi yapo timapita pamalo pampajha pochitila mapembhelo, tidakomana ni mbowa mmojhi wa mkazi uyo wadali ni chiwanda. Mwali mmeneyo wadali ni mzimu woombeza mkati mwake, uwo umampacha nghongono za kuombeza yayo siyachokele mchogolo. Mnamwali mmeneyo wamapacha opata ndalama zambili kwa njhito yake ya kuombeza. 17 Mwali mmeneyo wadamchata Poolo ni ife malo yonjhe yayo timapita, uku niwakweza mvekelo, pokamba, "Wandhu anyiyawa ni atumwi wa Mnungu wa mkulu! Akukambilani umo mukhoza kuomboledwa!"

Veja também