Poolo ni Sila aikidwa mndende
16 Siku limojhi yapo timapita pamalo pampajha pochitila mapembhelo, tidakomana ni mbowa mmojhi wa mkazi uyo wadali ni chiwanda. Mwali mmeneyo wadali ni mzimu woombeza mkati mwake, uwo umampacha nghongono za kuombeza yayo siyachokele mchogolo. Mnamwali mmeneyo wamapacha opata ndalama zambili kwa njhito yake ya kuombeza. 17 Mwali mmeneyo wadamchata Poolo ni ife malo yonjhe yayo timapita, uku niwakweza mvekelo, pokamba, "Wandhu anyiyawa ni atumwi wa Mnungu wa mkulu! Akukambilani umo mukhoza kuomboledwa!" 18 Wadayendekela kukamba chimwecho kwa masiku yambili mbaka mawu yake yadamkwiicha Poolo. Poolo wadang’anamuka ni kuchinyindila chijha chiwanda niwakamba, "Kwa mbhavu za Yesu Kilisito, nikulamula uchoke mkati mwake!" Pampajha chijha chiwanda chidamchoka.
19 Mambuye ayujha mwali yapo adaona chimwecho, adajhiwa kuti chikhulupi chao chopata ndalama chatha. Adaagwila Poolo ni Sila ni kwaakwekweta mbaka ku malo yayo wandhu amakomanilani kwa njhito za kila mtundu. 20 Wadaapeleka Poolo ni Sila pachogolo pa alamuli aku Loma ni kukamba, "Wandhu anyiyawa ni Ayahudi, ayambicha mkangano mmujhi mwathu. 21 Ayaluza kalidwe ilo ife wandhu a ku Loma sitiloledwa kuuvomela kapina kulichita." 22 Gulu lonjhe la wandhu lidalunjana kwaahundukila Poolo ni Sila.
Ndiipo wajha alamuli amilandu adalamula avulidwe njhalu zao ni kukwapulidwa vikwapu. 23 Yapo adamaliza kwabula kupunda, adaikidwa mndende. Achogoleli adaakambila alonda, "Mwaalonde wandhu anyiyawa zenezene." 24 Wamkulu wa ndende yapo wadavela yameneyo, wadaaika Poolo ni Sila mchumba cha mkhati kupunda mwa ndende ni kwaamanga mmiyendo yao pingu ya mbao.
25 Usiku pakati Poolo ni Sila amapembhela ni kumuimbila Mnungu nyimbo za matamando uku omangwidwa wina niwavechela. 26 Kudaveka mvekelo wa chimtingiza mndhaka, icho chidatingiza msingi wa ndende. Pampajha vicheko vidachakuka kwamkamojhi, ni maunyolo yajha adamangidwa omangidwa ameneo yadamasuka ni kugwa panjhi. 27 Yujha mlonda wa ndende yapo wadauka ni kuona vicheko vandende vachekuka, wamaganiza andende athawa, chimwecho wadasolomola upanga wake kuti wajhiphe. 28 Nambho Poolo wadamtana kwa mvekelo waukulu niwakamba, "Usadajhipa pakuti ife taonjhe tili muno!"
29 Yujha mlonda wa ndende wadatanicha nyali, ndiipo wadalowa msanga mkati mwa ndende mujha, wadajhitaya pachogolo pa Poolo ni Sila uku nawatendhemela kwa mandha. 30 Ndiipo wadaatulucha kubwalo ni kukamba, "Olemekezeka nichite chiyani kuti niomboledwe?"
31 Anyiiwo adamuyangha, "Akhulupilile Ambuye Yesu Kilisito, iwe pamojhi ni wandhu amnyumba mwako nde yapo siuomboledwe." 32 Chimwecho Poolo ni Sila adamlalikila uthenga wa Ambuye, yujha mlonda pamojhi ni wandhu wonjhe yao amakhala mnyumba mwake. 33 Ndhawi imweiijha yujha mlonda wa ndende wadaatenga Poolo ni Sila ni kwaachuka mabala yao. Ndiipo yujha mlonda pamojhi ni wandhu wonjhe amnyumba mwake adabatizidwa. 34 Wadaatenga Poolo ni Sila mbaka kukhomo kwake, wadaapacha chakudya. Iye Pamojhi ni wandhu amnyumba mwake adachita pwandho ndande chipano amkhulupilila Mnungu.
35 Umawa wake alamuli aku Loma wadaatuma asikali waakulu kwa wamkulu wa ndende akakambe, "Amasule ni uwasiye wandhu achameneo ajhipita."
36 Yujha wamkulu wa ndende wadamkambila Poolo, "Alamuli atuma uthenga kuti nikusiyeni, chimwecho chokani, mapitani kwa mtendele."
37 Nambho Poolo wadamkambila asikali, "Ukamba chiyani! Anyiwajha alamuli siadaone cholakwa chilichonjhe icho tachita, nambho atibula mikwapulo pandhandala popande kutilamula. Ata chimwecho ife ni wandhu aku Loma. Nao afuna kuti tichoke kwa chisisi. Siikhozeka, asiyeni ajhepano atituluche kubwalo!"
38 Wakulu wa sikali wajha adabwela ni kwaakambila anyiwajha alamuli mawu yajha wadakamba Poolo. Yapo adavela kuti Poolo ni Sila ni wandhu aku Loma, adaopa kupunda. 39 Chimwecho adapita kwaapepecha, ndiipo wadaachocha mndende ni kwaapembha kuti achoke kubwalo kwa ujha mujhi. 40 Poolo ni Sila adachoka mndende, adapita ku khomo kwa Lidiya, uko adakomana ni wajha wandhu adamkhulupalila Kilisito, adaathila mtima, ndiipo adachoka.