Pular para o conteúdo
Publicidade

Atos 2

Petulo wayaluza wandhu

14 Petulo wadaima pamojhi ni wajha atumwi khumi ni mmojhi, wadakweza mvekelo wake ni kwauzila gulu la wandhu lijha, niwakamba, "Ayahudi anjanga ni wandhu wonjhe yawo mkhala mu Yelusalemu, mlindile nikukambileni ni anyiimwe mnivechele bwino mawu yanga. 15 Zenedi wandhu anyiyawa siadalojhele ngati umo muganizila, pakuti saa zino kukali saa tatu umawa! 16 Nambho uzene nikuti chindhu ichi nde chijha chidakambidwa ni mlosi Yoeli, niwakamba,

17 Ambuye Amnungu akamba, Pa masiku yothela,

sinapache wandhu wonjhe Mzimu wanga.

Wana wanu ni anamwali wanu sialosele,

anyamata wanu saone maloso,

azee wanu saalote maloto.

18 Yetu ata mbowa zanga waachimuna ni waachikazi,

sinapache Mzimu wanga pa masiku yameneyo,

anyiiwo siachoche ulosi.

19 Sinichite vodabwicha kumwamba

ni vodabwicha pajhiko la panjihi.

Sikukhale mwazi, moto ni uchi waukulu.

20 Jhuwa silikhale mdima,

mwezi siukhale wofiwila ngati mwazi,

likali osafika siku lijha lalikulu ni laulemelelo la Ambuye.

21 Nambho, waliyonjhe uyo siwapembhele kwa jhina la Ambuye siwaomboledwe."

22 "Anyiiwme wandhu a ku Izilaeli vechelani mawu yaya niyakamba. Yesu wa ku Nazaleti wadali mundhu uyo wadachimikizidwa kwanu ni Mnungu kupitila vodabwicha, vozizicha ni vizindikilo, ivo Mnungu wadavichita pakati panu kupitila iye, ngati umo mwachinawene wake mujhiwila. 23 Kuyambila mmayambo Mundhu wadafuna anyiimwe mumphe Yesu, ni anyiimwe mdampha kwa kwasiila wandhu woipa ampachike pamtanda. 24 Nambho Mnungu wadamhyukicha ni kumchocha kupweteka kwa nyifa. Pakuti siidakhozeke kuti mbhavu za nyifa zimmange iye ngati mundhu womangidwa mndende. 25 Pakuti Daudi wadamkambilila Yesu chimwechi,

Nidaaona Atate pachogolo panga masiku yonjhe,

Ndande yake Iye wali kujhanja langa la kwene, sinitingizika.

26 Chimwecho, mtima wanga wajhazidwa ni chikondwelelo,

lilime langa likondwela kupunda,

thupi langa nalo silikhale kwa chiyembekezo.

27 Chifuko imwe Ambuye Amnungu simunisiya mu jhiko la wandhu akufa,

simumusiya mbowa wanu wopatulika kuwolela mchiliza.

28 Mwanilangiza njila iyo inichogoza kuumoyo, simunijhaze chimwemwe kwa kukalapo kwanu."

29 Abale wanga a Izilaeli, nifuna nikukambileni kwa kulimba mtima pamaso panu kuti mbuye wathu Daudi wadafa nikuikidwa mmanda, ni manda yake yakalipo mbaka lelo. 30 Iye wadali mlosi ni wadajhiwa icho Mnungu wadamuahidi iye. Mnungu wadamuahidi kwa kulumbila kuti mundhu mmojhi wa mbadwa wa Daudi siwakhale mfumu ngati umo wadali Daudi. 31 Daudi wadaona yayo siwachite Mnungu mchogolo, ndiipo wadakamba nghani za nyifa ya Yesu,

Siwadasiidwe mujhiko la wandhu akufa,

thupi lake silidaolele mu manda.

32 Mnungu ndeuyo wadamuhyukicha Yesu mmeneyo, ni ife taonjhe ni amboni anghani imeneyo. 33 Ngati Yesu walemekezedwa kwa kuikidwa ku jhanja la kwene la Mnungu, walandila Mzimu Woyela ngati umo adaahidi Atate. Chipano Yesu watipacha ife Mzimu Woyela, pa kumpacha kila mmojhi ngati umo muonela ni kuvela.

34 "Daudi mwene wake siwadakwele kumwamba, nambho iye mwene wake wadakamba,

Ambuye wadaakambila Ambuye wanga,

Khala pano pa jhanja langa la kwene

35 mbaka yapo sinaike adani wako kukhala paulamulilo wako."

36 "Chipano, wandhu wonjhe a mu Izilaeli ajhiwe zene kuti, Yesu uyo anyiimwe mudampachika pamtanda, Amnungu amchita kukhala Mbuye ni Kilisito muomboli."

37 Wandhu yapo adaevela chimwecho adavela kupwetekeka mmitima yawo ni adamfunjha Petulo ni anyiwajha atumwi anjake, "Achabale wathu, tichite chiyani?"

38 Petulo wadaayangha, "Lapani, kila mmojhi wanu mmbatizidwe kwa jhila la Yesu Kilisito, kuti mlekeleledwe machimo yanu ni kulandila ahadi ijha ya Mzimu Woyela. 39 Pakuti ahadi iyi ni ya anyiimwe pamojhi ni achanawanu ni kwa anyiwajha wonjhe ali kutali ni wandhu wonjhe yawo atanidwa ni Ambuye Mnungu wathu."

40 Petulo wadaaonya pakukamba mawu yambili ni kwaapembha niwakamba, "Mjhipenyelele ni mbadwa uwu woipa." 41 Wandhu ambili adakhulupilila mawu ya Petulo ni adabatizidwa, wandhu ngati elufu zitatu adawonjezekela pa gulu lawo siku limenelo.

Veja também