37 Papajha mwela waukulu udachokela, ni mafunde yadalibula lijha boti wadalimo Yesu mbaka lidayamba kujhala majhi. 38 Yesu wadali kumbuyo kwa lijha boti wadatogonela philo, oyaluzidwa wake adamuucha ni kumkambila, "Oyaluza, simganizila kuti ife titobila?"
39 Ndiipo Yesu wadauka ni kuunyindila mwela, "Khala chete!" Pampajha mwela udasiya ni nyanja idagona.
40 Chimwecho Yesu wadaakambila oyaluzidwa wake, "Ndande yanji muopa? Bwanji, mkali mlibe chikulupililo?"
41 Oyaluzidwa wake adaopa kupunda, adafunjhana, "Mundhu wa mtundu wanji uyu mbaka mwela umvela?"