9 Yapo wadamaliza kukamba chimwecho, Yesu wadanyakulidwa kupita kumwamba uku wonjhe naapenya, ni mtambo udamvinikila kuti saadamuonanjho.
10 Maso yawo yapo yadali yakali kumpenyechecha kumwamba Yesu yapo wamapita, mwachizulumukila wachimuna awili yawo adavala njhalu zoyela adaima pambhepete pawo, 11 adakamba, "Anyiimwe wandhu a ku Galilaya, ndande yanji muima pamenepo uku nimpenya kumwamba? Yesu uyo watengedwa kupita kumwamba, siwajhenjho ngati mujha mwamuwonela niwapita kumwamba."