Yesu wamlamicha mudhu wosapenye Batimayo
46 Ndiipo, adafika ku Yeliko. Yesu ni oyaluzidwa wake pamojhi ni gulu lalikulu la wandhu, adampheza mundhu mmojhi wosapenya, uyo wamatanidwa Batimayo, mwana wa Timayo, wakhala pambhepete pa njila niwapembha pembha vindhu. 47 Batimayo yapo wadavela kuti Yesu wa ku Nazaleti wamapita pamalo yameneyo, wadakweza mvekelo wake, niwakamba, "Imwe a Yesu, Mwana wa Daudi nilengeleni lisungu!" 48 Wandhu ambili adamnyindila, adamkambila wakhale chete, nambho iye wadapunda kukweza mvekelo, "Imwe Mwana wa Daudi, nilengeleni lisungu"
49 Yesu wadaima, ni kukamba "Mkambileni wajhe." Ndiipo adamtana, adamkambila, "Jhipache mtima, ima watokutana." 50 Niiye wadataya kutali njhalu yake, wadalumbha ni kumpitila Yesu.
51 Yesu wadamfunjha, "Ufuna nikuchitile chiyani?" Sapenya yujha wadamuyangha, "Oyaluza, nipemhba nipenye."
52 Yesu wadamkambila, "Pita, kukhulupilila kwako kwakulamicha." Pampajha, yujha sapenya wadakhoza kupenya, ndiipo wadamchata Yesu mnjila.