3 Pamenepo, adafika wandhu anayi, adamtenga mundhu wovuwala, adampeleka kwa Yesu. 4 Saadakhoze kumpeleka pafupi ni Yesu ndande ya lijha gulu la wandhu. Chimwecho adakwela pamwamba, adafulumula chindu, pajha wadali Yesu. Yapo adafulumula, adamchicha mundhu yujha uku amgoneka pa chitala. 5 Yesu yapo wadaona chikhulupililo chao, wadamkambila yujha mundhu wovuwala, "Bwenji langa, nakulekelela machimo yako." 6 Woyaluza akumojhi athauko la Musa, yawo adali pamenepo adaganizila mmitima yao, 7 "Chindhu chanji icho chimkhozecha kukamba chimwechi? Wamkafula Mnungu! Ni Mnungu yokha uyo wakhoza kulekelela machimo." 8 Pampajha, Yesu wadayajhiwa yayo amaganizila mmitima yao, wadaakambila, "Bwanji mganiza chimwecho? 9 Nichiti chili chopepuka kupunda, kumkambila mundhu uyu wavuwala, ‘Walekeledwa machimo yako,’ kapina kumkambila, ‘Uka, utenge chitala chako upite?’ 10 Chipano, nifuna mjhiwe kuti ine Mwana wa Mundhu nali ni ulamulilo wolekelela machimo ya wandhu pajhiko." Pamenepo, wadamkambila yujha mundhu wadavuwala, 11 "Nikukambila, uka utenge chitala chako, upite kukhomo!"
12 Pampajha yujha wodwala wadauka, wadatenga chitala chake ni kuchoka, uku wandhu wonjhe niampenya. Wandhu wonjhe adazizwa ni kumtamanda Mnungu, niakamba, "Sitidaonepo chindhu ngati ichi."