Achaabale auzene a Yesu
31 Amake ni achabale wake Yesu adafika pamenepo, adaima kubwalo, adamtuma mundhu mkati kuti wakamtane Yesu. 32 Gulu la wandhu lidamzungulila Yesu. Nawo wandhu wajha adamzungulila adamkambila, "Amako ni achabale wako ali kubwalo, atokufuna iwe." 33 Yesu wadaafunjha, "Maye wanga ni achabale wanga ni achiyani?" 34 Pamenepo wadaapenya wandhu wajha adamzungulila ni kukamba, "Penyani, anyiyawa nde maye wanga ni achabale wanga auzene. 35 Mundhu waliwonjhe uyo wachita yayo wayafuna Mnungu, mmeneyo nde mkulu wanga ni mlongowanga ni maye wanga."