Yesu waapacha chakudya wandhu elufu zisano
30 Anyiwajha atumwi adabwela kuchokela uko adatumidwa, ni adasonghana pachogolo pa Yesu, niadamkambila yonjhe yayo adayachita ni yajha amayaluza. 31 Yesu wadaakambila, "Tiyeni ife tekha pamalo yapo palibe wandhu, kuti tikapumulile pang’ono." Wadakamba chimwecho ndande kudali ni wandhu ambili kupunda yawo amajha pamenepo ni kuchoka, mbaka Yesu ni oyaluzidwa wake siamakhoze kupata ndhawi ya kudya chakudya ndande ya kwatumikila. 32 Ndiipo, adachoka okha kwa boti ni kupita kumalo yapo padalibe wandhu.
33 Nambho wandhu ambili yapo wadaona niachoka, adajhiwa uko apita. Chimwecho, wandhu ambili adachokela mmijhi yosiyanasiyana, adathamanga ni kwachogolela kufika. 34 Yesu yapo wadachika mboti, wadaliona gulu lalikulu la wandhu, wadaalengela lisungu ndande adali ngati mbelele zilibe owesa. Chimwecho wadayamba kwayaluza vindhu vambili. 35 Ujhulo yapo udajha, oyaluzidwa adamchata Yesu, adamkambila, "Pamalo pano ni paphululu, ni jhuwa litobila. 36 Waakambile wandhu apite mminda ni mvijhijhi va pafupi akajhigulile chakudya." 37 Nambho Yesu wadaakambila, "Mwachinawene wake mwapache chakudya." Ni anyiiyo adamfunjha, "Bwanji, tipite kugula mabumunda ya dinali miyambili ni kwapacha wandhu adye?" 38 Yesu waadafunjha, "Mli ni mabumunda yangati? Pitani mkapenye, mkaiwelenge." Yapo adawelenga, adamkambila, "Yalipo mabumunda yasano ni njhomba ziwili."
39 Ndiipo, Yesu wadaakambila oyaluzidwa wake, waakambile wandhu akhale magulu mgulu pamachamba yayawisi. 40 Chimwecho adakhala magulu ya wandhu miya ni ya wandhu amsini. 41 Ndiipo, Yesu wadayatenga yajha mabumunda yasano ni zijha njhomba ziwili, wadapenya kumwamba, wadamuyamika Mnungu, ndiipo wadayadula yajha mabumunda. Wadaapacha oyaluzidwa wake kuti wagawile wandhu. Chinchijha wadagawila wandhu zijha njhomba ziwili. 42 Wandhu wonjhe adadya ni kukhuta. 43 Ndiipo oyaluzidwa wake adatondola vidufya va mabumunda ni njhomba ivo vidakhalila, ni adajhaza miseche khumi ni iwili. 44 Wachimunape yawo adadya yajha mabumunda adali ngati elufu zisano.