Kujha kwa Mzimu Woyela
1 Yapo lidafika siku la pwando la Pentekosite, wandhu wonjhe yawo adamkhulupilila Yesu adasonghana malo yamojhi. 2 Mwachizulumukila mvekelo waukulu ngati mkokomo wa mbhepo udachoka kumwamba ni kuijhaza nyumba yonjhe mujha adakhala wajha atumwi. 3 Kudatulukila malilime ya moto yayo yadagawika ni kukhala pamwamba pa kila mmojhi wawo. 4 Wandhu wonjhe adajhazidwa ni Mzimu Woyela, adayamba kukamba mikambo ya chilendo, ngati umo wadafunila Mzimu Woyela.
5 Ndiipo kudali Ayahudi yawo amakhala mu Yelusalemu, yawo adachokela ku maiko yonjhe ya pajhiko lapanjhi.