Pular para o conteúdo
Publicidade

Marcos 11

Yesu walowa ku Yelusalemu kwa chikondwelo

1 Yesu ni oyaluzidwa wake yapo adafika ku Yelusalemu, ku vijhijhi va Besifage ni ku Besania, pafupi ni phili la Mizeituni, wadaatuma oyaluzidwa wake awili amchogolele. 2 Wadaakambila, "Pitani kukijhijhi chili pachogolo panu. Yapo simmalowe mmenemo, simpheze mwana wa phunda, uyo siwadatumike ni mundhu waliyonjhe. Mmasuleni ni mjhenayo. 3 Ngati mundhu wakakufunjhani ndande yanji mummasula, myangheni kuti Ambuye atomfuna ni sambweze chipanoyapa."

4 Anyiwajha oyaluzidwa adachoka, ni adampheza mwana wa phunda wamangidwa pafupi ni pakhomo la nyumba, mbhepete mwa njila. Yapo amammasula, 5 wandhu wina yawo adali pamenepo, adaafunjha, "Mchita chiyani? Ndande yanji mummasula mwana wa phundayo?" 6 Oyaluzidwa wajha adayangha ngati umo Yesu wadaakambila, ni wandhu achamenewo adaasiya apitenayo. 7 Adampeleka yujha mwana phunda kwa Yesu. Adayala njhalu zao pamsana pa yujha mwana punda, ni Yesu wadakwela pamsana ni kukhala. 8 Wandhu ambili adayala njhalu zao mnjila, ni wina adadula ndhawi zazing’onozingono za mitengo adaziyala mnjila ndande ya kumlemekeza Yesu. 9 Wandhu wonjhe adamchogolela ni anyiwajha amamchata mmbuyo, adakweza mvekelo niakamba, "Mtamandeni Mnungu! Wapachidwe mwawi uyo wakujha kwa jhina la Ambuye! 10 Mnungu waupache mwawi Ufumu uwo ukujha wa atate wathu mfumu Daudi. Watamandidwe Mnungu uyo wali kumwamba kupunda."

11 Yesu wadalowa kumujhi wa ku Yelusalemu ni kupita mbaka kunyumba ya Mnungu, wadapenyechecha kila chindhu. Nambho, ndande jhuwa lidabila, wadapita ku Besania pamojhi ni anyiwajha oyaluzidwa wake khumi ni awili.

Veja também