Pular para o conteúdo
Publicidade

Marcos 11

Yesu wauleswa mtengo wa mtini

12 Umawa wake yapo amachoka ku Besania kupita ku Yelusalemu, Yesu wadali ni njala. 13 Wadauona mtengo wa mtini kwa patali, uwo udali ni machamba yambili. Wadauchata kuti wapenye ngati wakhoza kupheza chipacho chalichonjhe. Nambho yapo wadauwandikila, wadauona ulibe chipacho chalichonjhe, nambho udali ni machamba yokha, pakuti nyengo ya yobala vipacho idali ikali. 14 Yesu wadaukambila ujha mtengo wa mtini, "Kuyambila lelo mbaka muyaya, siubalanjho." Ni oyaluzidwa wake adamvela yapo wadakamba chimwecho.

Veja também