11 Nambho anyiimwe muyaluza ngati mundhu uyo wali ni chindhu chakwaathangatila atate wake ni amake, nambho mkamba, ‘Thandizo ilo nidakupachani ni Kolobani’ mate yake chindhu ichi chapatulidwa ndande ya kumchochela Mnungu, 12 kwakuyaluza chimwecho mwachekeleza wandhu, siwadathangatila atate wao kapina amao. 13 Chimwecho, ndeumo mulidelela mawu la Mnungu ndande ya makhalidwe yanu yayo mudayalandila. Ni mchita vindhu vambili va mtundu umeneo."
Vindhu ivo vimchita mundhu siwadavomelezeka kwa Mnungu
14 Yesu wadalitananjho lijha gulu la wandhu, ni kulikambila, "Mnivechele mwaonjhe kuti mjhiwe. 15 Palibe chindhu chilowa mkati mwa mundhu kuchokela kubwalo icho chikhoza kumchita siwadavomelezeka kwa kumlambila Mnungu. Nambho icho chichoka mkati mwa mundhu ndeicho chimchita mundhu siwadavomelezeka kwa kumlambila Mnungu.