Pular para o conteúdo
Publicidade

Marcos 9

17 Mundhu mmojhi kuchokela mgulu la wandhu, wadamuyangha Yesu, "Oyaluza, nakupelekelani mwana wanga kwanu, wali ni chiwanda icho chamchita wakhale bubu. 18 Ndhawi yaliyonjhe yapo chimzamwa chimtaya panjhi ni kumchita wachoke ni matovu mkamwa, ni kutafuna mano yake, ni watouma thupi lake. Nidaapembha oyaluzidwa wako amchoche chiwanda chimenecho, nambho siadakhoze."

19 Yesu wadaakambila, "Anyiimwe mbadwa ulibe chikhulupililo, sinikhale ni anyiimwe mbaka siku liti? Sinikulimbileni mtima mbaka siku lanji? Majhanayoni pano mwana mmeneyo." 20 Chimwecho adampeleka kwa Yesu yujha wadali ni chiwanda.

Pampajha, chijha chiwanda yapo chidamwona Yesu, chidamchita wakhale ni njili, wadangwa panjhi, wadawalauka ni kuchocha matovu mkamwa. 21 Yesu wadamfunjha tate wayujha mwana, "Bwanji, utenda uwu wampata kuyambila siku lanji?" wadamuyangha, "Kuyambila yapo wadali mwana. 22 Ninyengo za mbili chiwanda chimenecho chimgwecha pamoto ni pamajhi, kuti chimphe. Nambho, ngati mkhoza kuchita chindhu, tilengele lisungu, utithangatile!" 23 Yesu wadamkambila, "Ngati uli ni chikhulupililo, yonjhe yakhozeka kwa uyo wakhulupilila." 24 Pampajha, tate wa yujha mwana wadalila kwa mvekelo, "Nikhulupilila! Nambho chikhulupililo changa chaching’ono, nithangatileni kuti nikhoze kukhulupilila."

25 Yesu yapo wadaona gulu la wandhu lichuluka kwa chisanga, wadachinyindila chijha chiwanda, "Iwe chiwanda umchita uyu mundhu kukhala wosakamba ni wosavela, nikulamula mchoke mnyamata uyu ni siudamlowanjho!" 26 Pampajha, chijha chiwanda chidatutuma ni kumgwecha njili ni kumchoka. Mwana yujha wadaoneka ngati wamwalila, ni wandhu ambili adakamba, "Wathomwalila!" 27 Nambho Yesu wadamgwila jhanja mnyamata yujha, wadamthangatila kunyakuka, nayo wadanyakuka.

Veja também