Pular para o conteúdo
Publicidade

João 14

16 Sinaapembhe Atate nawo sakupacheni Wakukuthandizani mwina, uyo siwakhale namwe muyaya. 17 Iye ni Mzimu wa zene. Jhiko lapanjhi silikhoza kumlandila ndande silimuona kapina kumjhiwa. Nambho anyiimwe mumjhiwa ndande wakhala namwe ni wali mkati mwanu."

18 "Sinikusiyani amasiye, sinijhenjho kwanu. 19 Ikali ndhawi yochepa wandhu ajhiko la panjhi sanionanjho, nambho anyiimwe simunione, pakuti ine nili wamoyo namwenjho simukhale moyo. 20 Ndhawi ijha ikafika simujhiwe kuti ine nilimkati mwa Atate, namwe muli mkati mwanga ni ine nilimkati mwanu."

21 "Uyo wayalandila malamulo yanga ni kuyagwila, mmeneyo nde uyo wanikonda. Uyo wanikonda ine siwakondedwe ni Atate wanga, nane sinimkonde ni kujhijhiwicha kwa iye."

22 Chimwecho Yuda nambho osati Isikaliyote adamkambila, "Ambuye, sikhozeke bwanji mujhilangize kwa ife ni osati kwa jhiko?"

23 Yesu wadayangha, "Wandhu yao anikonda akalichitila njhito mawu langa ni Atate wanga saakonde, nafe sitijhe kwa anyiiwo ni kukhala pamojhi nawo. 24 Uyo siwanikonda siwayachitila njhito mawu yanga. Uthenga uwo muuvela osati wanga nambho uchokela kwa Atate yao anituma."

25 "Nikuyaluzani vindhu ivi nikali pamojhi namwe, 26 nambho Othandiza, Mzimu woyela, uyo samtume kukhala mmalo mwanga, siwakuyaluzeni kila kandhu ni kukukumbuchani yonjhe yayo nakukambilani."

Veja também