Yesu wabatizidwa ni kuyesedwa
9 Ndhawi imeneyo Yesu wadachokela mmujhi wa Nazaleti, mujhiko la Galilaya, wadafika kwa Yohana, nayo wadambatiza mumchinje Yolodani. 10 Yesu yapo wadachuuka mmajhi, pamwepo wadaona kumwamba kwamasulidwa, ni Mzimu Woyela udamchikila ngati nghunda.