45 Malembo yalembedwa, "Mundhu woyamba Adamu wadali choumbidwa chamoyo" Nambho Adamu wothela iye ni Mzimu uyo wapacha wandhu umoyo. 46 Nambho lichogolela kukhalako, opande thupi lijha la chizimu ila thupi la kawaida, ndiipo likujha thupi lijha la chizimu. 47 Mundhu woyamba yaani Adamu, wadaumbidwa kwa dothi, wadachoka mndhaka, mundhu wakawili yaani Kilisito wadachoka kumwamba. 48 Wonjhe ali ajhiko la panjhi ali ngati mundhu uyo wadaumbidwa kwa dothi, anyiwajha ali akumwamba ali ngati yujha wadachoka kumwamba. 49 Ngati mujha talingana ni yujha wadaumbidwa kwa dothi, chimwecho ndeumo sitilingane ni yujha wachoka kumwamba.