Pular para o conteúdo
Publicidade

1 Akolinso 7

12 Nambho kwa wina, ine nikukambilani osati Ambuye akamba, ngati wammuna wali ni wamkazi, siwada khulupilile, ni wamkazi wavomela kukhala nayo siwadamsiya. 13 Wamkazi uyo wamkhulupilila Kilisito, ngati wali ni wammuna uyo siwadakhulupilile, niwammuna mmeneyo wavomela kukhala nayo siwadamsiya. 14 Kwa wammuna siwadakhulupile walandilidwa kwa Mnungu kwa kulunjana ni mkazake, ni wamkazi siwada khulupilile walandilidwa ni Mnungu kwa kulunjana ni wammuna wamkhulupilila Kilisito. Ngati siidakali chimwecho wana wanu sadakavomelezedwa ni Mnungu, kumbe chipano avomelezedwa kukhala wana a Mnungu.

Veja também